Mawu a M'munsi
a Agiriki ankakonda kwambiri maphunziro apamwamba. Plutarch, amene anakhala ndi moyo nthawi imodzi ndi Timoteyo, analemba kuti: “Maphunziro apamwamba ndi gwero ndi muzu wa zinthu zonse zabwino. . . . Ndi maphunziro amenewa, amene amathandiza munthu kukhala ndi makhalidwe abwino kwambiri komanso chimwemwe. . . . Zinthu zina zonse ndi zopanda phindu ndi zachabechabe ndipo palibe chifukwa chovutikira nazo.”—Moralia, I, “The Education of Children.”