Mawu a M'munsi
a Aamoni anali anthu ankhanza kwambiri. Patapita zaka pafupifupi 60 kuchokera nthawi imeneyi, anaopseza kukolowola diso lakumanja la munthu wina aliyense wokhala m’mudzi wina wa ku Gileadi. Mneneri Amosi ananenaponso kuti anthu amenewa nthawi ina anatumbula akazi apakati a ku Gileadi.—1 Samueli 11:2; Amosi 1:13.