Mawu a M'munsi
a Jonatani anali wazaka zosachepera 20 pamene anatchulidwa koyamba monga woyang’anira gulu lankhondo, chakumayambiriro kwa ulamuliro wa zaka 40 wa Sauli. (Numeri 1:3; 1 Samueli 13:2) Motero, pamene Jonatani ankamwalira cha m’ma 1078 B.C.E., ayenera kuti anali ndi zaka pafupifupi 60. Popeza kuti panthawiyi Davide anali ndi zaka 30, zikuoneka kuti Jonatani ankasiyana zaka pafupifupi 30 ndi Davide.—1 Samueli 31:2; 2 Samueli 5:4.