Mawu a M'munsi
a Nsanja ya Olonda ya September 1, 1983, pamasamba 31 ndi 32, ili ndi mfundo zimene mwamuna ndi mkazi wake ayenera kuziganizira. Mwa zina, magaziniyi inati: “Adzachita bwino kukulitsa chidani pa chinthu chirichonse chimene chiri chodetsedwa pamaso pa Yehova, kuphatikizapo mikhalidwe imene mwachiwonekere iri yoluluza ya kugonana. Awiri okwatirana ayenera kuchita mwa njira imene idzawasiya ali ndi chikumbu mtima choyera . . . akumakumbukira makamaka kuti kugonana kuyenera kukhala kolemekezeka, kosaluluzika, chisonyezero cha chikondi chokoma mtima. Zimenezi zowonadi siziyenera kuphatikiza chirichonse chimene chikanyansa kapena kubvulaza mnzake wa mu ukwati wa munthuyo.—Aefeso 5:28-30; 1 Petro 3:7.”