Mawu a M'munsi
a Mawu a Yesu amenewa akutithandiza kuchotsa maganizo olakwika a mmene Mabaibulo ena anamasulirira mawu akuti “kukhalapo.” Mabaibulo ena anamasulira mawuwa kuti “kubwera,” kapena “kubweranso,” zimene zimatanthauza zochitika za kanthawi kochepa. Komano, onani kuti Yesu sanayerekezere nthawi ya kukhalapo kwake ndi Chigumula cha m’tsiku la Nowa, chomwe chinangochitika kamodzi, koma anayerekezera ndi “masiku a Nowa,” omwe anali nthawi yaitali. Mofanana ndi nthawi ya kale imeneyi, kukhalapo kwa Khristu ndi nthawi yaitali imene anthu adzakhala otanganidwa kwambiri ndi zinthu zochitika tsiku ndi tsiku moti sadzatha kulabadira chenjezo.