Mawu a M'munsi
b Khoti limeneli (The European Court of Human Rights) ndi nthambi ya bungwe lina la ku Ulaya (Council of Europe) ndipo cholinga chake ndi kuonetsetsa kuti anthu sakuphwanya mfundo zimene anagwirizana pa msonkhano wina waukulu woona za ufulu wa anthu. Dziko la Georgia linasaina nawo panganoli pa May 20, 1999. Motero linavomereza kuti lizitsatira mfundo za kumsonkhanowu.