Mawu a M'munsi
a Munthu wosusuka amakhala ndi maganizo aumbombo ndipo amadya mosadziletsa. Choncho, amaonekera osati ndi kunenepa kwa munthu koma ndi mmene munthuyo amaonera chakudya. Munthu atha kukhala wochepa thupi kapena wowonda koma ali wosusuka. Nthawi zina munthu amatha kukhala wonenepa chifukwa cha matenda kapena chibadwa chake. Komabe, kaya munthu ndi wonenepa kapena wowonda, nkhani yagona pa dyera la munthuyo pankhani ya chakudya.—Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2004.