Mawu a M'munsi
a N’zochititsa chidwi kuti Yona anachokera m’tauni ya ku Galileya chifukwa choti, ponyoza Yesu Afarisi ananena kuti: “Fufuza ndipo sudzapeza pamene pamati m’Galileya mudzatuluka mneneri.” (Yohane 7:52) Omasulira mabuku ndiponso ofufuza ambiri amati ponena mawu amenewa, Afarisi anali kutanthauza kuti m’mbuyomo kapena panthawiyo panalibiretu mneneri aliyense amene anachokera m’chigawo chonyozeka cha Galileya. Ngati izi n’zimene Afarisiwo anali kutanthauza ndiye kuti iwo anali kuthawa dala chilungamo chifukwa mawu amenewa anali otsutsana ndi mbiri komanso ulosi wa m’Baibulo.—Yesaya 9:1, 2.