Mawu a M'munsi
b Davide analinso ngati mwana wa nkhosa amene amakhulupirira mbusa wake. Iye ankadalira Mbusa Wamkulu, Yehova, kuti amuteteze ndi kumutsogolera. Ndi chidaliro chonse, iye anati: “Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa” kanthu. (Sal. 23:1) Yohane Mbatizi ananena kuti Yesu ndi “Mwanawankhosa wa Mulungu.”—Yoh. 1:29.