Mawu a M'munsi
a Magazi, omwe Mulungu amawaona kuti ndi opatulika, ndi omwe ankathandiza kuti iye akhululukire munthu machimo ake. (Levitiko 17:11) Ndiyeno kodi zimenezi zikusonyeza kuti nsembe za ufa zimene anthu osauka ankapereka zinali zopanda ntchito? Ayi, chifukwa Yehova ankaona kuti anthu omwe ankapereka nsembe zotere ankasonyeza kudzichepetsa komanso kumvera. Ndiponso machimo a Aisiraeli onse, kuphatikizapo omwe anali osauka, ankakhululukidwa chifukwa cha magazi a nyama zomwe zinkaperekedwa nsembe kwa Mulungu chaka chilichonse pa Tsiku la Chitetezo.—Levitiko 16:29, 30.