Mawu a M'munsi
a Dzina la gulu lampatuko limeneli (Gnostic) linachokera ku mawu a Chigiriki amene angatanthauze kuti “nzeru zachinsinsi,” ndipo dzina la mabukuwo (Apocrypha) linachokera ku mawu otanthauza “zobisidwa mosamala.” Masiku ano kuli mabuku achinyengo kapena kuti osayenera kukhala m’Baibulo amene analembedwa moyerekezera mabuku a Uthenga Wabwino, buku la Machitidwe, makalata a atumwi ndiponso buku la Chivumbulutso. Ena amati mabukuwa ndi owonjezera pa Malemba Achigiriki Achikhristu, koma palibe umboni wotsimikizira zimenezi.