Mawu a M'munsi
a Dzina lakuti Yehova limapezeka pafupifupi maulendo 7,000 m’mipukutu yoyambirira ya Baibulo. Dzinali limatanthauza kuti “Ine ndine yemwe ndili ine.” (Eksodo 3:14) Mulungu angathe kukhala chilichonse chimene iye wafuna n’cholinga chakuti akwaniritse cholinga chake. Choncho, dzina limeneli limasonyeza kuti Mulungu nthawi zonse amachita zofuna zake ndiponso kuti chilichonse chimene amalonjeza chimachitika.