Mawu a M'munsi
b Ngakhale kuti Baibulo limanena kuti Yehova ‘anatseka mimba ya Hana,’ palibe umboni wosonyeza kuti Mulungu sankasangalala ndi Hana, yemwe anali mkazi wokhulupirika komanso wodzichepetsa. (1 Samueli 1:5) Baibulo nthawi zina limanena kuti Mulungu wachititsa chinachake, koma kwenikweni amakhala kuti wangolola kuti zichitike.