Mawu a M'munsi
b Pamenepa, Petulo sanali kunena za dziko lapansi lenilenili. Mose, yemwe analemba nawo Baibulo, anagwiritsanso ntchito mawu akuti “dziko lapansi” mophiphiritsa. Iye anati: “Dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi.” (Genesis 11:1) Dziko lapansi lenilenili si limene limalankhula “chinenedwe chimodzi.” Mofananamo, si dziko lenilenili limene lidzawonongedwe. M’malo mwake, mogwirizana ndi zimene Petulo ananena, amene adzawonongedwe ndi anthu osaopa Mulungu.