Mawu a M'munsi
b Chihema chopatulika chinali cha makona anayi, ndipo chinali chongopangidwa ndi matabwa amene anawaphimba ndi chinsalu chachikulu. Koma ngakhale zinali choncho, chihema chopatulikachi anachimanga pogwiritsa ntchito zipangizo zapamwamba kwambiri monga zikopa za akatumbu, nsalu zopetedwa mokongola kwambiri ndiponso matabwa amtengo wapatali okutidwa ndi siliva ndi golide. Kunja kwa chihemachi kunali bwalo limenenso linali la makona anayi. M’bwalomo munalinso guwa lansembe lokongola kwambiri. Zikuoneka kuti patapita nthawi anamanganso zipinda zina za ansembe m’bwalomo. Samueli ayenera kuti ankagona m’chimodzi cha zipinda zimenezi.