Mawu a M'munsi
c Nkhani imeneyi imanena zinthu ziwiri zopanda ulemu zimene ana a Eli ankachita. Chilamulo chinaneneratu zigawo za nyama yoperekedwa nsembe zimene ansembe anayenera kudya. (Deuteronomo 18:3) Koma kuchihemako, ansembe oipa amenewo anayamba kuchita zawozawo. Iwo ankauza anthu owathandizira kuti azipisa ndi chifoloko chachikulu m’miphika ya nyama imene inali pamoto ndipo ankatenga nyama iliyonse imene akufuna. Komanso anthu akabweretsa nsembe zawo kuchihema kuti azipereke paguwa la nsembe, ansembe oipawo ankachititsa owathandizira awo kuchitira chipongwe anthu odzapereka nsembewo. Ankachita zimenezi pokakamiza anthu kuti aziwapatsa nyama yosaphika ngakhale asanapereke mafuta a nyamayo ngati nsembe kwa Yehova.—Levitiko 3:3-5; 1 Samueli 2:13-17.