Mawu a M'munsi
b Azimayi ambiri amavutika maganizo kwa milungu yochepa akangobereka kumene. Koma ena amadwala matenda enaake ovutika maganizo amene azimayi omwe angobereka kumene amadwala. Kuti mudziwe zimene mungachite pofuna kuzindikira komanso kuthana ndi matenda amenewa, werengani nkhani yakuti “Ndinagonjetsa Vuto Langa Losokonezeka Maganizo Nditabereka,” mu Galamukani! ya August 8, 2002, ndi yakuti “Understanding Postpartum Depression,” mu Galamukani! yachingerezi ya June 8, 2003. Magazini amenewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mungawerengenso nkhani zimenezi m’Chingelezi pa Intaneti pogwiritsa ntchito adiresi iyi, www.jw.org.