Mawu a M'munsi
d Chaka cha ulamuliro wa mafumu a ku Babulo chinkayamba m’mwezi wa Nisani ndipo chinkathanso m’mwezi wa Nisani. Ngati mfumu yamwalira isanamalize chakachi, mfumu yotsatira inkayamba kulamulira kuti imalizitse chakacho m’malo mwa mfumu yomwalirayo. Chaka chimene zimenezi zachitika chinkatchedwa “chaka cholowera ufumu” cha mfumu yatsopanoyo. Motero, chaka choyamba cha ulamuliro wa mfumu yatsopanoyo, chinkayamba m’mwezi wotsatira wa Nisani.