Mawu a M'munsi
b Mulungu amadana ndi zothetsa banja mwachinyengo kapena popanda zifukwa zomveka. Ngati wina wachita chigololo, Mulungu amapereka mwayi kwa wosalakwayo wothetsa banjalo ngati akufuna. (Malaki 2:16; Mateyu 19:9) Onani nkhani yakuti “Lingaliro la Baibulo—Kodi Nkusudzula kwa Mtundu Wotani Kumene Mulungu Amada?” m’Galamukani! ya February 8, 1994, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.