Mawu a M'munsi
a Matendawa alipo a mitundu ingapo ndipo amakhudza mbali ya ubongo imene imathandiza kuti manja ndi miyendo zizigwira ntchito. Matendawa amapangitsanso kuti munthu azidwala matenda akugwa, azivutika kudya komanso azilephera kulankhula. Mtundu wa matenda amene Jairo amadwala ndi woopsa kwambiri ndipo umachititsa kuti manja ndi miyendo ziume komanso kuti khosi lake likhale lawedewede.