Mawu a M'munsi
a Mwachitsanzo nthawi ina Aisiraeli anagonjetsedwa ndi Aamaleki komanso Akanani, chifukwa anakamenyana nawo Mulungu asanawalamule. (Numeri 14:41-45) Kenako patadutsa zaka zambiri, Yosiya yemwe anali Mfumu, anachitanso zomwezi. Zimene anachitazi zinachititsa kuti ataye moyo wake.—2 Mbiri 35:20-24.