Mawu a M'munsi
b Aisiraeli sanalengeze mfundo za mtendere asanakamenyane ndi Akanani chifukwa choti Akananiwo anali okanika. Anali atapatsidwa nthawi yokwanira yoti asinthe makhalidwe awo oipa. Koma ayi ndithu sanasinthe, moti pa nthawi imene Aisiraeli ankabwera kuti amenyane nawo, makhalidwe awo anali ataipiratu. (Genesis 15:13-16) Choncho Aisiraeli ankafunika kuseseratu Akanani onse kupatulapo anthu amene anasintha makhalidwe awo.—Yoswa 6:25; 9:3-27.