Mawu a M'munsi
a Pa nkhani imeneyi, pulofesa wina analemba kuti akatswiri ambiri amaganiza kuti pamene Yesu anati “lero” ankatanthauza kuti adzakhala m’paradaiso pa tsiku lomwelo la maola 24. Koma pulofesayu ananenanso kuti: “Kukhala ndi maganizo amenewa pa nkhaniyi kumavuta chifukwa Baibulo limasonyeza kuti Yesu ataphedwa ‘anatsikira’ kaye m’manda (Mat. 12:40; Mac. 2:31; Aroma 10:7) ndipo kenako anapita kumwamba.”