Mawu a M'munsi
a Kodi tidzakhalabe okhulupirika kwa Yehova kapena tidzalola kuti Satana atisokoneze? Yankho la funso limeneli silidalira kukula kwa mayesero amene tingakumane nawo koma mmene tikutetezera mtima wathu. Kodi mawu akuti “mtima” amatanthauza chiyani? Kodi Satana angasokoneze bwanji mtima wathu? Nanga tingatani kuti tiuteteze? Mafunso amenewa ayankhidwa munkhaniyi.