Mawu a M'munsi
b TANTHAUZO LA MAWU ENA: Yehova anatipatsa luso loti tizitha kufufuza maganizo athu, mtima wathu komanso zochita zathu n’kumadziweruza. M’Baibulo luso limeneli limatchedwa chikumbumtima. (Aroma 2:15; 9:1) Chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo chimagwiritsa ntchito mfundo za Yehova, zomwe zimapezeka m’Baibulo, kuti chiziweruza ngati zimene timaganiza, kuchita kapena kulankhula zili zabwino kapena ayi.