Mawu a M'munsi
a Akhristufe tapatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu komanso kuphunzitsa anthu. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti tikwaniritse mbali zonse za utumiki wathu ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto. Tikambirananso zimene tingachite kuti tizilalikira mogwira mtima komanso mosangalala.