Mawu a M'munsi
c MAWU OFOTOKOZERA ZITHUNZI: Chithunzichi chikusonyeza zimene zingadzachitike pa “chisautso chachikulu.” Abale ndi alongo angapo akubisala m’chipinda cham’mwamba. Popeza amagwirizana, akulimbikitsana kwambiri pa nthawi yovutayo. Abale ndi alongowa anali atayamba kale kugwirizana chisautso chachikulu chisanayambe.