Mawu a M'munsi
a Tikukhala m’dziko lomwe wolamulira wake ndi Satana yemwe ndi tate wake wa bodza. Choncho nthawi zambiri zimativuta kuti tiziyendabe m’choonadi. Nawonso Akhristu a munthawi ya atumwi ankakumana ndi vuto lomweli. Pofuna kuwathandiza komanso kutithandiza ifeyo, Yehova anauzira mtumwi Yohane kulemba makalata atatu. Mfundo za m’makalatawa zitithandiza kudziwa zinthu zimene zingachititse kuti tisiye kuyenda m’choonadi komanso zomwe tingachite kuti tisagonje.