Mawu a M'munsi
c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Zithunzi zitatu zosonyeza zimene zikuchitika misonkhano isanayambe, ikuchitika komanso itatha. 1: Mkulu akupereka moni mwansangala kwa mlendo, m’bale wachinyamata wanyamula maikofoni komanso mlongo wachitsikana akucheza ndi mlongo wachikulire. 2: Ana komanso achikulire akweza manja kuti ayankhe paphunziro la Nsanja ya Olonda. 3: Banja likugwira nawo ntchito yoyeretsa m’Nyumba ya Ufumu. Mayi akuthandiza mwana wake kuti aponye ndalama m’bokosi. M’bale wachinyamata akusamalira mabuku komanso m’bale wina akulimbikitsa mlongo wachikulire.