Mawu a M'munsi
a Kuphunzitsa kumatanthauza kuthandiza munthu kuti ayambe “kuganiza komanso kuchita zinthu m’njira yatsopano kapena kuti mosiyana ndi mmene amachitira poyamba.” Lemba lathu lachaka cha 2020, la Mateyu 28:19, limatikumbutsa kufunika kophunzira Baibulo ndi anthu n’kuwathandiza kuti afike pobatizidwa n’kukhala ophunzira a Yesu Khristu. Munkhaniyi komanso yotsatira, tikambirana zimene tingachite kuti tizigwira bwino ntchito yofunika kwambiri imeneyi.