Mawu a M'munsi
a Mwamuna akakwatira, amakhala mutu wa banja lake. Munkhaniyi tikambirana zimene kukhala mutu kumatanthauza, chifukwa chake Yehova anakonza zoti ena azikhala ndi udindo wotsogolera komanso zimene amuna angaphunzire kwa Yehova ndi Yesu. Munkhani yotsatira, tidzaona zimene amuna ndi akazi angaphunzire kwa Yesu komanso anthu ena otchulidwa m’Baibulo. Ndipo munkhani yachitatu, tidzakambirana zimene abale angachite kuti azigwiritsa ntchito moyenera udindo wawo mumpingo.