Mawu a M'munsi
a Yehova anaonetsa mneneri Zekariya masomphenya osiyanasiyana ochititsa chidwi. Zimene Zekariya anaona zinathandiza iyeyo komanso anthu a Mulungu kupeza mphamvu zowathandiza kulimbana ndi mavuto omwe ankakumana nawo, pomwe ankabwezeretsa kulambira koona. Masomphenyawo angatithandizenso ifeyo kutumikira Yehova mokhulupirika ngakhale tikukumana ndi mavuto. Munkhaniyi tikambirana mfundo zofunika zomwe tingaphunzire pa masomphenya a Zekariya okhudza choikapo nyale ndi mitengo ya maolivi.