Mawu a M'munsi
a Pa Deuteronomo 23:3-6, lamulo la Mulungu linkanena kuti a Amoni ndi a Mowabu asamalowe mu mtundu wa Aisiraeli. Koma zikuoneka kuti lamuloli linkaletsa kuti anthu a mitundu imeneyi asamavomerezedwe mwalamulo kukhala Aisiraeli, koma silinkawaletsa kuchita zinthu ndi Aisiraeli kapenanso kukhala pakati pawo. Onani buku la Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 95.