Mawu a M'munsi
d Mfumu Asa anachita machimo aakulu. (2 Mbiri 16:7, 10) Koma Baibulo limasonyeza kuti Yehova ankamuona kuti anachita zabwino. Ngakhale kuti poyamba anakana atadzudzulidwa, n’kutheka kuti pambuyo pake analapa. Koma zabwino zimene anachita ndi zambiri tikayerekezera ndi zimene analakwitsa. Chofunika kwambiri ndi chakuti Asa ankalambira Yehova yekha ndipo anayesetsa kuchotsa mafano mu ufumu wake.—1 Maf. 15:11-13; 2 Mbiri 14:2-5.