Mawu a M'munsi
a Aisiraeli ambiri omwe anaona zodabwitsa zimene Yehova anachita pa Nyanja Yofiira, sanakalowe m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 14:22, 23) Yehova analamula kuti anthu a zaka 20 kapena kuposa pamenepo adzafera m’chipululu. (Num. 14:29) Koma Yoswa, Kalebe, anthu ambiri a fuko la Levi ndi ena onse amene anali asanakwanitse zaka 20 anakhalabe ndi moyo ndipo anaona Yehova akukwaniritsa lonjezo lake pamene Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodano n’kukalowa m’dziko la Kanani.—Deut. 1:24-40.