Mawu a M'munsi
a Pa nthawiyi, M’bale Peter Vanderhaegen ndi M’bale Len Davis, omwe anachita umishonale kwa zaka zambiri m’dzikoli, anali atapitirira zaka 60, moti dziko la Indonesia silinkawaonanso ngati amishonale. Komanso Mlongo Marian Tambunan (yemwe poyamba anali Marian Stoove) anali atakwatiwa ndi mwamuna wa ku Indonesia konko. Choncho anthu atatu onsewa analoledwa kukhalabe m’dzikoli. Onse anakhalabe okhulupirika ndipo ngakhale kuti ntchito yolalikira inali yoletsedwa, anthuwa sanasiye kulalikira.