Mawu a M'munsi
a M’Baibulo, mawu amene anamasuliridwa kuti “dipo” amanena za malipiro kapena chinthu chimene chimaperekedwa pogula zinthu. Mawu achiheberi akuti, ka·pharʹ amatanthauza “kuphimba.” Nthawi zambiri mawuwa amanena za kuphimba machimo. (Salimo 65:3, mawu a m’munsi) Mawu ena ofanana nawo akuti koʹpher amatanthauza malipiro amene amaperekedwa kuti awombole chinachake. (Ekisodo 21:30) Mawu achigiriki akuti lyʹtron omwe nthawi zambiri amamasuliridwa kuti “dipo” angatanthauzenso “malipiro owombolera” chinthu. (Mateyu 20:28; Baibulo lakuti, The New Testament in Modern Speech, lolembedwa ndi R. F. Weymouth) Anthu olemba mabuku m’Chigiriki ankagwiritsa ntchito mawu akuti lyʹtron ponena za malipiro amene ankaperekedwa kuti munthu wogwidwa pa nkhondo kapena kapolo amasulidwe.