Mawu a M'munsi
a Chakumayambiriro kwa chaka cha 2020, Komiti ya Ogwirizanitsa inavomereza kuti misonkhano yampingo iziulutsidwa pa TV ndi pa wailesi m’madera ena pa nthawi ya mliri wa COVID-19. Inavomereza zimenezi pofuna kuthandiza anthu amene sangapange misonkhano pogwiritsa ntchito foni kapena intaneti chifukwa choti zinthuzi sizipezeka kwawo kapena ndi zodula kwambiri moti sangakwanitse. Koma kumadera kumene anthu amatha kulumikizana ndi mpingo wawo pogwiritsa ntchito intaneti sayenera kugwiritsa ntchito njira imeneyi.