Lachinayi, October 23
Muzike mizu ndiponso mukhale okhazikika pamaziko.—Aef. 3:17.
Monga Akhristu, sitimangokhutira ndi kumvetsa mfundo zoyambirira za m’Baibulo. Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, timafunitsitsanso kudziwa “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:9, 10) Bwanji osakonza zoti mufufuze mozama zinthu zomwe zingakuthandizeni kuti mukhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Mwachitsanzo, mungafufuze mmene anasonyezera kuti ankakonda atumiki ake akale komanso mmene zimenezo zimasonyezera kuti inunso amakukondani. Mungaphunzirenso zimene Yehova ankafuna kuti Aisiraeli azichita pomulambira n’kuziyerekezera ndi zimene amafuna kuti ifenso tizichita pomulambira masiku ano. Kapenanso mungaphunzire mozama zokhudza maulosi amene Yesu anakwaniritsa pa utumiki wake padziko lapansi. Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani lingakuthandizeni kuti muzisangalala pophunzira. Kuphunzira Baibulo mozama kungalimbitse chikhulupiriro chanu komanso kungakuthandizeni kuti ‘mumudziwedi Mulungu.’—Miy. 2:4, 5 w23.10 18-19 ¶3-5
Lachisanu, October 24
Koposa zonse, muzikondana kwambiri chifukwa chikondi chimakwirira machimo ochuluka.—1 Pet. 4:8.
Mawu amene mtumwi Petulo anagwiritsa ntchito akuti “muzikondana kwambiri,” angatanthauze “kutambasula.” Mbali yachiwiri ya vesili ikufotokoza zotsatira za chikondi chimenechi. Ikuti chimakwirira machimo ochuluka a abale athu. Zili ngati timagwira chikondichi ndi manja awiri ngati mmene tingagwirire nsalu, n’kuchitambasula kuti chiphimbe, osati machimo ochepa, koma “machimo ochuluka.” Mawu akuti kuphimba, kapena kuti “kukwirira,” akufotokoza za kukhululuka. Mofanana ndi nsalu yomwe ingaphimbe malo akuda pa chovala, chikondi chimaphimba zimene abale athu amalakwitsa. Tiyenera kumakonda kwambiri abale athu moti tikhoza kuwakhululukira zolakwa zawo, ngakhale pamene kuchita zimenezi kungakhale kovuta. (Akol. 3:13) Tikakhululukira ena timasonyeza kuti timawakonda kwambiri komanso timafuna kusangalatsa Yehova. w23.11 11-12 ¶13-15
Loweruka, October 25
Safani anayamba kuwerengera mfumu bukulo.—2 Mbiri 34:18.
Atakula, Mfumu Yosiya anayamba kukonzanso kachisi. Pogwira ntchitoyi “anapeza buku la Chilamulo cha Yehova loperekedwa ndi dzanja la Mose.” Mfumuyi itamva zimene zinawerengedwa, nthawi yomweyo inasintha kuti itsatire malangizo a m’bukuli. (2 Mbiri 34:14, 19-21) Kodi mumafuna kuti muziwerenga Baibulo tsiku lililonse? Ngati mukuyesa kale kuchita zimenezi kodi zinthu zikukuyenderani bwanji? Kodi mumasunga mavesi ena ake omwe mukuona kuti angakuthandizeni? Yosiya ali ndi zaka pafupifupi 39, analakwitsa zinthu ndipo zinachititsa kuti aphedwe. Iye anadzidalira m’malo mopempha malangizo kwa Yehova. (2 Mbiri 35:20-25) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kaya ndife wamkulu kapena wamng’ono kapenanso takhala tikuphunzira Baibulo kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tiyenera kupitiriza kufunafuna Yehova. Zimenezi zikuphatikizapo kupempha Yehova nthawi zonse kuti atipatse malangizo, kuphunzira Mawu ake komanso kumvera malangizo a Akhristu olimba mwauzimu. Tikamachita zimenezi tidzapewa kulakwitsa kwambiri zinthu ndipo tidzakhala osangalala.—Yak. 1:25. w23.09 12 ¶15-16