Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
Chilengezo
Chinenero chatsopano chomwe chilipo: Mbum
  • Lero

Lamlungu, July 27

[Muzitha] kulimbikitsa . . . ndiponso kudzudzula.—Tito 1:9.

Kuti mukhale Mkhristu wolimba mwauzimu muyenera kuphunzira maluso amene angakuthandizeni. Malusowa angakuthandizeni kuti mukwaniritse bwino maudindo anu mumpingo, mupeze ntchito kuti muzipeza zofunika pa moyo wanu kapena wa banja lanu komanso kuti muzigwirizana ndi anthu ena. Mwachitsanzo, muziphunzira kuwerenga ndi kulemba bwino. Baibulo limanena kuti munthu amene amawerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku n’kumawaganizira mozama, amakhala wosangalala ndipo zinthu zimamuyendera bwino. (Sal. 1:1-3) Munthu akamawerenga Baibulo tsiku lililonse, amadziwa maganizo a Yehova ndipo izi zimamuthandiza kuti aziganiza bwino komanso azitsatira mfundo za m’Malemba. (Miy. 1:3, 4) Abale ndi alongo athu amafuna kuthandizidwa ndi amuna odziwa kuphunzitsa komanso kupereka malangizo ochokera m’Baibulo. Ngati mumawerenga komanso kulemba bwino, mukhoza kukonzekera ndemanga komanso nkhani zimene zingapindulitse anthu ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chawo. Mungathenso kulemba notsi zimenezi zingakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu komanso kulimbikitsa anthu ena. w23.12 26-27 ¶9-11

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lolemba, July 28

Amene ali wogwirizana ndi inu ndi wamkulu kuposa amene ali wogwirizana ndi dziko.​—1 Yoh. 4:4.

Mukamachita mantha, muziganizira zimene Yehova adzachite m’tsogolo, Satana akadzachotsedwa. Pamsonkhano wachigawo wa 2014, panali chitsanzo cha zimene tingachite poganizira za chiyembekezo chathu. Mu chitsanzocho, bambo ankakambirana ndi banja lake mmene lemba la 2 Timoteyo 3:1-5 lingamvekere ngati mavesiwa atakhala kuti akufotokoza mmene zidzakhalire m’Paradaiso. Anawerenga kuti: “M’dziko latsopano, idzakhala nthawi yapadera komanso yosangalatsa. Pakuti anthu adzakhala okonda anzawo, okonda kulambira Mulungu, odzichepetsa, ofatsa, otamanda Mulungu, omvera makolo, oyamikira, okhulupirika, okonda achibale awo, ofuna kugwirizana ndi anzawo, onena zabwino za anzawo, odziletsa, odekha, okonda zabwino, odalirika, oganizira za ena, osadzitukumula ndiponso osanyada, okonda Mulungu, m’malo mokonda zosangalatsa, ndiponso odziperekadi kwa Mulungu. Anthu amenewa usasiyane nawo.” Kodi mumakambirana ndi anthu a m’banja lanu kapena anzanu mmene moyo udzakhalire m’dziko latsopano? w24.01 6 ¶13-14

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lachiwiri, July 29

Umandisangalatsa kwambiri.—Luka 3:22.

N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amasangalala ndi anthu ake onse monga gulu. Baibulo limati: “Yehova amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Komabe nthawi zina ena angamakayikire n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova amasangalala ndi ineyo pandekha?’ Ambiri mwa atumiki okhulupirika a Yehova akale nthawi zinanso ankavutika ndi maganizo ngati amenewa. (1 Sam. 1:6-10; Yobu 29:2, 4; Sal. 51:11) Baibulo limasonyeza kuti anthu omwe si angwiro akhoza kusangalatsa Yehova. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kukhulupirira Yesu Khristu komanso kubatizidwa. (Yoh. 3:16) Tikatero timasonyeza poyera kuti talapa machimo athu ndipo talonjeza kuti tizichita zimene Mulungu amafuna. (Mac. 2:38; 3:19) Yehova amasangalala akaona tikuchita zimenezi n’cholinga choti tikhale naye pa ubwenzi. Iye amasangalala nafe n’kumationa ngati anzake apamtima tikamapitiriza kuchita zimene tingathe pokwaniritsa zimene tinalonjeza podzipereka.—Sal. 25:14. w24.03 26 ¶1-2

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena