Lachiwiri, July 29
Umandisangalatsa kwambiri.—Luka 3:22.
N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amasangalala ndi anthu ake onse monga gulu. Baibulo limati: “Yehova amasangalala ndi anthu ake.” (Sal. 149:4) Komabe nthawi zina ena angamakayikire n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi Yehova amasangalala ndi ineyo pandekha?’ Ambiri mwa atumiki okhulupirika a Yehova akale nthawi zinanso ankavutika ndi maganizo ngati amenewa. (1 Sam. 1:6-10; Yobu 29:2, 4; Sal. 51:11) Baibulo limasonyeza kuti anthu omwe si angwiro akhoza kusangalatsa Yehova. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tiyenera kukhulupirira Yesu Khristu komanso kubatizidwa. (Yoh. 3:16) Tikatero timasonyeza poyera kuti talapa machimo athu ndipo talonjeza kuti tizichita zimene Mulungu amafuna. (Mac. 2:38; 3:19) Yehova amasangalala akaona tikuchita zimenezi n’cholinga choti tikhale naye pa ubwenzi. Iye amasangalala nafe n’kumationa ngati anzake apamtima tikamapitiriza kuchita zimene tingathe pokwaniritsa zimene tinalonjeza podzipereka.—Sal. 25:14. w24.03 26 ¶1-2
Lachitatu, July 30
Ife sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.—Mac. 4:20.
Tingatsanzire ophunzira a Yesu, popitiriza kulalikira ngakhale pamene akuluakulu a boma aletsa ntchito yathu. Ifenso tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatithandiza kuti tikwaniritse utumiki wathu. Choncho tizimupempha kuti atithandize kukhala olimba mtima komanso atipatse nzeru. Tizimupemphanso kuti atithandize kupirira mavuto. Ambirife tikukumana ndi mavuto okhudza thanzi kapena maganizo, imfa ya okondedwa athu, mavuto a m’banja, kuzunzidwa kapenanso mavuto ena. Ndipo zinthu monga miliri komanso nkhondo zachititsa kuti zikhale zovuta kwambiri kulimbana ndi mavutowa. Choncho muzipemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. Muzimuuza zimene zikuchitika pa moyo wanu ngati mmene mungachitire ndi mnzanu wapamtima. Muzikhulupirira kuti Yehova “adzachitapo kanthu.” (Sal. 37:3, 5) Kulimbikira kupemphera kungatithandize ‘kupirira mavuto.’ (Aroma 12:12) Yehova amadziwa zimene zikuchitikira atumiki ake ndipo ‘amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.’—Sal. 145:18, 19. w23.05 5-6 ¶12-15
Lachinayi, July 31
Nthawi zonse muzitsimikizira kuti chovomerezeka kwa Ambuye nʼchiti.—Aef. 5:10.
Tikafuna kusankha zochita pa nkhani zikuluzikulu, tiyenera “kuzindikira chifuniro cha Yehova” n’kuchita zinthu mogwirizana ndi zimenezo. (Aef. 5:17) Tikapeza mfundo za m’Baibulo zogwirizana ndi mmene zinthu zilili kwa ifeyo timakhala kuti tapeza maganizo a Yehova pa nkhaniyo. Ndiyeno tikamagwiritsa ntchito mfundozo, timasankha zochita mwanzeru. Satana, yemwe ndi mdani wathu “woipayo,” amafuna kuti tizitanganidwa ndi zinthu zam’dzikoli n’cholinga choti tisakhale ndi nthawi yotumikira Mulungu. N’zosavuta kuti Mkhristu aziika patsogolo chuma, maphunziro kapena ntchito m’malo motumikira Yehova. (1 Yoh. 5:19) Zikatero, munthuyo amakhala kuti wayamba kuganiza ngati anthu a m’dzikoli. N’zoona kuti zinthu zimenezi pazokha si zolakwika koma siziyenera kukhala pamalo oyamba. w24.03 24 ¶16-17