Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Lero

Loweruka, September 13

Ndiwe munthu wokondedwa kwambiri.—Dan. 9:23.

Mneneri Danieli anali wachinyamata pamene Ababulo anamugwira monga kapolo n’kupita naye kudziko lakutali ndi kwawo. Anthuwo ayenera kuti anachita naye chidwi. Iwo anaona “zooneka ndi maso,” monga zakuti Danieli “analibe chilema chilichonse” ndiponso ankachokera m’banja lolemekezeka. (1 Sam. 16:7) Pa zifukwa zimenezi, Ababulo anamuphunzitsa kuti azikatumikira kunyumba yachifumu. (Dan. 1:3, 4, 6) Yehova ankakonda Danieli chifukwa cha zimene mnyamatayu anasankha kuti azichita pa moyo wake. Ndipotu n’kutheka kuti iye anali ndi zaka pafupifupi 20 zokha, pamene Yehova anamutchula pamodzi ndi Nowa komanso Yobu, amuna amene anatumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka zambiri. (Gen. 5:32; 6:9, 10; Yobu 42:16, 17; Ezek. 14:14) Danieli anakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali ndipo Yehova anapitiriza kumukonda kwa moyo wake wonse munthu wokhulupirikayu.—Dan. 10:11, 19. w23.08 2 ¶1-2

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lamlungu, September 14

[Muzitha] kumvetsa bwino mulifupi, mulitali, kukwera ndi kuzama kwa choonadi.​—Aef. 3:18.

Mukafuna kugula nyumba mungafune kudziwa kalikonse kokhudza nyumbayo. Tingachitenso zofanana ndi zimenezi pamene tikuwerenga komanso kuphunzira Baibulo. Ngati mutaliwerenga mofulumira, mukhoza kungodziwa “mfundo zoyambirira za m’mawu opatulika a Mulungu.” (Aheb. 5:12) Koma mofanana ndi zimene mungachite ndi nyumba ija, muyenera kulowa “mkati” kapena kuti kuliphunzira mosamala kuti mulimvetse. Njira yabwino kwambiri yophunzirira Baibulo ndi kuona mmene mbali zosiyanasiyana za uthenga wake zilili zogwirizana. Muziyesetsa kuti mumvetse, osati mfundo za choonadi zomwe mumakhulupirira zokha, koma chifukwa chakenso mumazikhulupirira. Kuti tizimvetsa bwino Mawu a Mulungu, tiyenera kumaphunzira mosamala mfundo zozama za choonadi. Mtumwi Paulo analimbikitsa abale ndi alongo ake kuti aziphunzira Mawu a Mulungu mwakhama n’cholinga choti ‘adziwe bwino mulifupi ndi mulitali ndi kukwera ndi kuzama’ kwa choonadi. Iwo akanachita zimenezi, ‘akanazika mizu ndi kukhala okhazikika’ m’chikhulupiriro chawo. (Aef. 3:14-19) Ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. w23.10 18 ¶1-3

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025

Lolemba, September 15

Abale, pa nkhani ya kumva zowawa ndi kuleza mtima, tengerani chitsanzo cha aneneri amene analankhula m’dzina la Yehova.​—Yak. 5:10.

M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe anali oleza mtima. Bwanji osakonza zoti mufufuze zitsanzozi pamene mukuphunzira Baibulo panokha? Mwachitsanzo, ngakhale kuti Davide anadzozedwa ali mwana kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli, anafunika kudikira kwa zaka zambiri asanapatsidwe ufumuwo. Simiyoni ndi Anna ankatumikira Yehova mokhulupirika pamene ankayembekezera kubwera kwa Mesiya. (Luka 2:25, 36-38) Mukamaphunzira nkhanizi muzifufuza mayankho a mafunso awa: Kodi n’kutheka kuti n’chiyani chinathandiza munthuyu kuti akhale woleza mtima? Kodi kukhala woleza mtima kunamuthandiza bwanji? Kodi ndingamutsanzire bwanji? Mungapindulenso ngati mutaphunzira za anthu omwe sanasonyeze kuleza mtima. (1 Sam. 13:8-14) Mungadzifunse kuti: ‘Kodi mwina n’chiyani chinachititsa kuti asakhale woleza mtima? Nanga zotsatirapo zake zinali zotani?’ w23.08 25 ¶15

Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
Takulandirani.
Laibulaleyi imathandiza anthu kufufuza mabuku ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova a m'zinenero zosiyanasiyana.
Kuti mupange dawunilodi mabuku, pitani pa jw.org.
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena