Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bi12 tsamba 1943-1944
  • 5 “Manda” Olembedwa ndi “M” Wamkulu Manda a Anthu Onse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 5 “Manda” Olembedwa ndi “M” Wamkulu Manda a Anthu Onse
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
5 “Manda” Olembedwa ndi “M” Wamkulu Manda a Anthu Onse

5 “Manda” Olembedwa ndi “M” Wamkulu Manda a Anthu Onse

Chiheberi, שאול (sheʼohlʹ); Chigiriki, ᾅδης (haiʹdes); Chilatini, in·ferʹnus; Chisiriya, shiul

Malo 66 Mmene Mukupezeka Sheʼohlʹ

Mawu achiheberi akuti sheʼohlʹ (Sheoli) ndi achigiriki akuti haiʹdes (hade) tawamasulira kuti “Manda” wokhala ndi “M” wamkulu kuti tiwasiyanitse ndi dzenje limodzi loikamo mtembo. Mawu achiheberi akuti sheʼohlʹ akupezeka malo 66 m’Malemba Achiheberi. Malo ake ndi awa: Ge 37:35; 42:38; 44:29, 31; Nu 16:30, 33; De 32:22; 1Sa 2:6; 2Sa 22:6; 1Mf 2:6, 9; Yob 7:9; 11:8; 14:13; 17:13, 16; 21:13; 24:19; 26:6; Sl 6:5; 9:17; 16:10; 18:5; 30:3; 31:17; 49:14, 14, 15; 55:15; 86:13; 88:3; 89:48; 116:3; 139:8; 141:7; Miy 1:12; 5:5; 7:27; 9:18; 15:11, 24; 23:14; 27:20; 30:16; Mla 9:10; Nym 8:6; Yes 5:14; [7:11]; 14:9, 11, 15; 28:15, 18; 38:10, 18; 57:9; Eze 31:15, 16, 17; 32:21, 27; Ho 13:14, 14; Amo 9:2; Yon 2:2 ndi Hab 2:5.

Malo amene sheʼohlʹ akupezeka m’Malemba Achiheberi akuphatikizapo malo 65 amene mawuwa akupezeka m’Malemba Achiheberi olembedwa ndi Amasorete, komanso malo amodzi pa Yes 7:11, pamene pali mawu akuti sheʼaʹlah, kutanthauza “funsa.” Koma akangosintha mavawelo ake pang’ono, ndiponso mogwirizana ndi Mabaibulo angapo akale, mawuwa amawalemba kuti sheʼoʹlah, kutanthauza “kulowera ku Manda” kapena “kupita ku Manda.” M’malo onse amene muli mawu achiheberi akuti sheʼohlʹ, Baibulo la Dziko Latsopano lawamasulira kuti “Manda” wokhala ndi “M” wamkulu. Baibulo lachigiriki la Septuagint m’malo ambiri linamasulira sheʼohlʹ ndi mawu akuti haiʹdes.

Ngakhale kuti pali mawu osiyanasiyana amene amaonedwa kuti n’kumene kunachokera mawu achiheberi akuti sheʼohlʹ, zikuoneka kuti mawuwa anachokera ku mawu achiheberi akuti שׁאל (sha·ʼalʹ), kutanthauza “kufunsa” kapena “kupempha.” Izi zingasonyeze kuti sheʼohlʹ ndi malo amene amapempha kapena kuitana anthu onse molamula komanso popanda kusankha, akamalandira anthu akufa amene akubwera kumalowa. Choncho sheʼohlʹ si mawu osonyeza mmene zinthu zilili kwa munthu. Malowa ali munthaka ndipo nthawi zonse amagwiritsidwa ntchito ponena za anthu akufa, ndiponso amangotanthauza manda a anthu onse, kapena munthaka mmene muli anthu akufa (osati m’nyanja). Mosiyana ndi zimenezi, mawu achiheberi akuti qeʹver amatanthauza dzenje limodzi la manda kapena kuti malo amene aikamo mtembo.—Ge 23:4, 6, 9, 20.

Malo 10 Mmene Mukupezeka Haiʹdes

Mawu achigiriki akuti haiʹdes, amene mwinamwake amatanthauza “malo osaoneka,” akupezeka m’malo 10 m’Malemba Achigiriki, pamavesi awa: Mt 11:23; 16:18; Lu 10:15; 16:23; Mac 2:27, 31 ndi Chv 1:18; 6:8; 20:13, 14. M’malo onsewa, Baibulo la Dziko Latsopano lagwiritsa ntchito mawu akuti “Manda,” wokhala ndi “M” wamkulu, pomasulira mawu achigiriki akuti haiʹdes.

Mawu a Petulo pa Mac 2:27, pamene anagwira mawu Sl 16:10 akusonyeza kuti haiʹdes n’chimodzimodzi ndi sheʼohlʹ ndipo amatanthauza Manda a anthu onse (kusiyana ndi mawu achigiriki akuti taʹphos, amene amatanthauza dzenje limodzi la manda). Mawu achilatini ofanana ndi haiʹdes ndi in·ferʹnus (nthawi zina amati inʹfe·rus). Mawuwa amatanthauza “chimene chili kunsi, dera la kunsi,” ndipo amanena za manda a anthu onse. Chotero sakusiyana kwenikweni ndi mawu achiheberi akuti sheʼohlʹ ndi achigiriki akuti haiʹdes.

M’Malemba ouziridwa, mawu akuti sheʼohlʹ ndi haiʹdes amagwiritsidwa ntchito pamene akunena za imfa ndi anthu akufa, osati moyo ndi anthu amoyo. (Chv 20:13) Mwa iwo okha, mawu amenewa sachititsa munthu kuganiza n’komwe za kusangalala kapena kumva kupweteka.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena