Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.*
58 Kodi mungalankhule bwanji za chilungamo mutakhala chete?+
Kodi mungaweruze mwachilungamo, inu ana a anthu?+
2 Ayi, mʼmalomwake mukuganiza zochita zinthu zopanda chilungamo mumtima mwanu,+
Ndipo mumalimbikitsa zachiwawa mʼdzikoli.+
3 Oipa amasochera* akangobadwa.*
Iwo amakhala osamvera komanso abodza kuchokera nthawi imene anabadwa.
4 Iwo ali ndi poizoni ngati wa njoka.+
Ndipo ndi ogontha ngati njoka ya mamba imene yatseka makutu ake.
5 Singamve mawu a anthu amatsenga,
Ngakhale atachita matsengawo mwaluso.
6 Inu Mulungu, agululeni mano mʼkamwa mwawo.
Inu Yehova, thyolani nsagwada za mikango* imeneyi.
7 Asowe ngati madzi amene akuyenda.
Mulungu akoke uta wake nʼkuwagwetsa ndi mivi yake.
8 Akhale ngati nkhono imene imasungunuka ikamayenda.
Ngati mwana wa mayi amene wapita padera, yemwe saona dzuwa.
9 Miphika yanu isanayambe kumva kutentha kwa moto wa mitengo yaminga,
Mulungu adzauluza mitengo yaiwisi komanso imene ikuyaka ngati ikuuluzika ndi mphepo yamkuntho.+
10 Wolungama adzasangalala chifukwa chakuti waona oipa akupatsidwa chilango.+
Mapazi ake adzaponda magazi a anthu oipa.+
11 Kenako anthu adzati: “Ndithudi wolungama amalandira mphoto.+
Ndithudi pali Mulungu amene amaweruza padziko lapansi.”+