Mutu 35
Kupha Babulo Wamkulu
1. Kodi mngelo ananena mawu otani pofotokoza chilombo chofiira kwambiri chija, ndipo pamafunika nzeru yotani kuti munthu amvetse zizindikiro za m’buku la Chivumbulutso?
MNGELO uja anapitiriza kufotokoza za chilombo chofiira kwambiri chotchulidwa pa Chivumbulutso 17:3, ndipo anauza Yohane kuti: “Apa m’pamene pakufunika kuchenjera ndiponso kukhala ndi nzeru: Mitu 7 ikuimira mapiri 7, amene mkazi uja amakhala pamwamba pake. Palinso mafumu 7. Asanu agwa, imodzi ilipo, inayo sinafikebe. Koma ikafika, ikufunika kudzakhala kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 17:9, 10) Apa mngeloyu anafotokoza nzeru yochokera kumwamba ndipo nzeru imeneyi ndi yokhayo imene ingathandize munthu kumvetsa zizindikiro za m’buku la Chivumbulutso. (Yakobo 3:17) Nzeruyi imathandiza Akhristu odzozedwa ndiponso anzawo kuti azindikire kufunika kwa nthawi imene tikukhalayi. Imathandiza anthu odzipereka kwa Mulungu kukhala ndi mtima woyamikira ziweruzo za Yehova zimene zatsala pang’ono kuperekedwa, ndiponso imawathandiza kuti aziopa Yehova moyenera. Zimenezi zikugwirizana ndi lemba la Miyambo 9:10, lomwe limati: “Kuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru. Kudziwa Woyera Koposa, ndiko kumvetsa zinthu.” Kodi nzeru yochokera kwa Mulungu imeneyi ikutiululira chiyani za chilombo chija?
2. Kodi mitu 7 ya chilombo chofiira kwambiri chija ikuimira chiyani, ndipo mawu akuti “asanu agwa, imodzi ilipo” akutanthauza chiyani?
2 Mitu 7 ya chilombo cholusachi ikuimira “mapiri” 7, kapena kuti “mafumu” 7. Mawu awiri onsewa amagwiritsidwa ntchito m’Malemba kuimira maboma olamulira. (Yeremiya 51:24, 25; Danieli 2:34, 35, 44, 45) Baibulo limatchula maulamuliro 6 amene anali amphamvu kwambiri padziko lonse, omwe anachita zinthu zosiyanasiyana zokhudza anthu a Mulungu. Maulamulirowa anali Iguputo, Asuri, Babulo, Mediya ndi Perisiya, Girisi, ndi Roma. Pa maulamuliro amenewa, 5 anali atalamulira kale pomafika nthawi imene Yohane ankaona masomphenya a m’buku la Chivumbulutso, ndipo ulamuliro wa Roma unali udakali ndi mphamvu kwambiri padziko lonse. Zimenezi zikugwirizana bwino kwambiri ndi mawu akuti, “asanu agwa, imodzi ilipo.” Nanga bwanji za mfumu “inayo,” yomwe inali isanafike?
3. (a) Kodi chinachitika n’chiyani kuti Ufumu wa Roma ugawanike? (b) Kodi m’chigawo Chakumadzulo cha Ufumu wa Roma munachitika zotani? (c) Kodi Ufumu Wopatulika wa Roma tiyenera kuuona bwanji?
3 Yohane atamwalira, Ufumu wa Roma unapitirizabe kukula ndipo unalamulirabe kwa zaka mahandiredi ambirimbiri. Mu 330 C.E., Mfumu Constantine anasamutsa likulu la ufumuwu kuchokera mumzinda wa Roma kupita ku Byzantium, ndipo anasintha dzina la mzindawu n’kukhala Constantinople. Ndipo mu 395 C.E., Ufumu wa Roma unagawanika pawiri, n’kukhala chigawo Chakum’mawa ndi Chakumadzulo. Kenako mu 410 C.E., mzinda wa Roma unagonjetsedwa ndi Alaric, yemwe anali mfumu ya anthu a fuko linalake (Visigoth) ochokera kudziko la Germany ndi mayiko ena oyandikana nalo. Anthu a fuko limeneli anakopedwa n’kuyamba kutsatira mfundo zimene ankati ndi zachikhristu, zomwe munthu wina dzina lake Arius anayambitsa. Mafuko enanso ochokera m’mayikowa, omwenso ankati ndi achikhristu, anagonjetsa dziko la Spain ndiponso dera lalikulu lomwe linali la Ufumu wa Roma kumpoto kwa Africa. Kwa zaka zambiri, m’mayiko a ku Ulaya munkachitika zinthu zosiyanasiyana, monga zipolowe, ziwawa ndiponso kusintha kwa olamulira. Olamulira ena otchuka anayamba kulamulira m’madera ena m’chigawo Chakumadzulo cha Ufumu wa Roma, monga Charlemagne, yemwe anachita mgwirizano ndi Papa Leo Wachitatu m’zaka za m’ma 800 C.E. Wolamulira wina anali Frederick Wachiwiri, yemwe analamulira m’zaka za m’ma 1200 C.E. Komabe, ngakhale kuti ufumu umene anthuwa ankalamulira unkatchedwa Ufumu Wopatulika wa Roma, madera ake anali ochepa poyerekeza ndi madera amene Ufumu wa Roma woyambirira unkalamulira utakula kwambiri. Ufumu wachiwiriwu sunali watsopano, koma unangokhala ngati ukukhazikitsanso kapena ukupitiriza ulamuliro wa ufumu woyambirira uja.
4. Kodi chigawo Chakum’mawa cha Ufumu wa Roma chinachita zinthu zotani zosonyeza kuti zinthu zinkayenda bwino ndithu m’chigawochi? Nanga n’chiyani chinachitikira madera ambiri a kumpoto kwa Africa, Spain, ndiponso Siriya, omwe anali a Ufumu wa Roma wakale?
4 Chigawo Chakum’mawa cha Ufumu wa Roma, chomwe likulu lake linali ku Constantinople, sichinkamwerana madzi ndi chigawo Chakumadzulo cha ufumuwu. Mwachitsanzo, m’ma 500 C.E., Justinian Woyamba, yemwe anali mfumu ya chigawo Chakum’mawa anagonjetsa ndi kulandanso dera lalikulu la kumpoto kwa Africa komanso analowerera dziko la Spain ndi Italy. M’zaka za m’ma 600 C.E., Justinian Wachiwiri analandanso madera a ku Makedoniya, omwe poyamba anali a ufumuwu koma analandidwa ndi anthu a mtundu wachisilavo. Koma pofika m’zaka za m’ma 700 C.E., madera akuluakulu omwe anali a Ufumu wa Roma wakale anali atayamba kulamulidwa ndi ufumu watsopano wachisilamu. Madera ake anali chigawo chakumpoto kwa Africa, Spain ndiponso Siriya. Ufumu watsopanowu unatenga maderawa m’manja mwa Ufumu wa Roma, womwe poyamba likulu lake linali mumzinda wa Roma koma kenako linasamukira mumzinda wa Constantinople.
5. Ngakhale kuti mzinda wa Roma unawonongedwa mu 410 C.E., n’chiyani chikusonyeza kuti panapita zaka zambiri kuti Ufumu wa Roma usiyiretu kulamulira madera onse?
5 Mzinda wa Constantinople unakhalapobe kwa zaka zambiri ndithu. Mzindawu unapulumuka maulendo ambirimbiri pamene unkaukiridwa pafupipafupi ndi Aperisiya, Aluya, anthu a ku Bulgaria, komanso anthu ochokera ku Russia. Pofika mu 1203, mzindawu unagonjetsedwa, osati ndi Asilamu, koma ndi asilikali omwe ankati ndi achikhristu ochokera m’chigawo Chakumadzulo. Komabe, mu 1453, mzindawu unayamba kulamuliridwa ndi Mehmed Wachiwiri, yemwe anali Msilamu wa mumzinda womwewo ndipo posapita nthawi, mzindawu unakhala likulu la Ufumu wa Ottoman, kapena kuti Turkey. Choncho, ngakhale kuti mzinda wa Roma unawonongedwa mu 410 C.E., panapita zaka zambiri kuti Ufumu wa Roma usiyiretu kulamulira madera onse. Ngakhale pamene unasiya kulamulira, anthu a m’mayiko omwe ankayendera mfundo za tchalitchi cha Katolika ndi cha Eastern Orthodox anapitirizabe kutsatira zinthu zomwe zinayambira mu ufumuwu.
6. Kodi ndi maufumu ati atsopano omwe anayamba, ndipo ufumu wamphamvu kwambiri unali uti?
6 Koma pofika m’zaka za m’ma 1400 C.E., mayiko ena anali atayamba kukhazikitsa maufumu atsopano. Ngakhale kuti ena mwa maufumu amenewa anakhazikitsidwa m’madera omwe poyamba ankalamuliridwa ndi Ufumu wa Roma, maufumuwa sankangopitiriza Ufumu wa Roma koma anali atsopano. Mwachitsanzo, mayiko a Portugal, Spain, France ndiponso Holland, anakhala maufumu amphamvu ndipo anagonjetsa madera ambiri akutali. Koma dziko la Britain ndi lomwe linakhala ufumu wamphamvu kwambiri ndipo linkalamulira mayiko ochuluka zedi, moti pa nthawi iliyonse zinkapezeka kuti kumalo enaake mu ufumuwu dzuwa silinalowe. Pa nthawi zosiyanasiyana, ufumuwu unkalamulira mayiko ambiri a ku North America, Africa, India, ndi kum’mwera chakum’mawa kwa Asia, komanso zilumba zambiri za ku South Pacific.
7. Kodi ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse wopangidwa ndi mayiko awiri unayamba bwanji, ndipo Yohane anati ulamulirowu, kapena kuti ‘mutu’ wa 7, ukhalapo kwa nthawi yaitali bwanji?
7 Pofika m’zaka za m’ma 1800, madera ena a ku North America omwe ankalamulidwa ndi Ufumu wa Britain anali atachoka mu ufumuwu ndipo anapanga dziko loima palokha la United States of America. Koma mayiko a Britain ndi United States of America anapitirizabe kukokanakokana. Komabe, nkhondo yoyamba yapadziko lonse inachititsa kuti mayikowa azindikire kuti ali ndi zolinga zofanana ndipo anagwirizana n’kuyambitsa ubale wapadera. Choncho ufumu wamphamvu kwambiri padziko lonse wopangidwa ndi mayiko awiri unakhazikitsidwa. Ufumuwu unapangidwa ndi dziko la United States of America, lomwe panopa ndi lolemera kwambiri padziko lonse, ndi la Great Britain, lomwe linali likulu la ufumu wamphamvu kwambiri padziko lonse. Motero, ufumu umenewu ndi ‘mutu’ wa 7, kapena kuti ufumu wa 7 wamphamvu kwambiri padziko lonse. Ufumuwu wafika mpaka m’nthawi ya mapeto ino komanso m’madera amene Mboni za Yehova zamasiku ano zinayambira. Tikayerekezera nthawi imene ufumuwu ulamulire, ndi nthawi yaitali imene mutu wa 6 unalamulira, mutu wa 7 umenewu ukhalapo kwa “kanthawi kochepa,” mpaka pamene Ufumu wa Mulungu udzawononge mayiko onse.
N’chifukwa Chiyani Chilombochi Chikutchedwa Mfumu ya 8?
8, 9. Kodi mngelo uja anati chilombo chophiphiritsa chofiira kwambiri chija n’chiyani, ndipo chinatuluka bwanji mwa mitu 7?
8 Mngelo uja anapitiriza kuuza Yohane kuti: “Ndipo chilombo chimene chinalipo, koma tsopano palibe, n’chimenenso chili mfumu ya 8, koma yotuluka mwa mafumu 7 aja, ndipo ikupita ku chiwonongeko.” (Chivumbulutso 17:11) Chilombo chophiphiritsa chofiira kwambirichi, ‘chinatuluka mwa’ mitu 7. Zimenezi zikutanthauza kuti chinachokera ku mitu ya ‘chilombo chotuluka m’nyanja’ choyambirira chija, chomwe chifaniziro chake ndi chilombo chofiira kwambirichi. Kodi chilombo chofiira kwambirichi chinatuluka motani mwa mitu 7? Mu 1919, ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse wa Britain ndi America ndi umene unali mutu womwe unkalamulira. Mitu 6 inali italamulira kale, ndipo tsopano ulamuliro wapadziko lonse unali m’manja mwa ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse wopangidwa ndi mitu iwiri imeneyi. Mutu wa 7 umenewu, womwe panopa ndi ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse, ndi umene unathandiza kwambiri kuti bungwe la League of Nations likhazikitsidwe. Komanso mutuwu ndi womwe ukuthandiza kwambiri bungwe la United Nations ndiponso kulipatsa ndalama zambiri. Choncho mophiphiritsa, chilombo chofiira kwambiri chija, chomwe ndi mfumu ya 8, ‘chinatuluka mwa’ mitu 7 yoyambirira ija. Tikaganizira masomphenyawa mwanjira imeneyi, mawu akuti chinatuluka mwa mitu 7 akugwirizana bwino kwambiri ndi masomphenya ena a m’mbuyomu. Masomphenyawo ndi akuti chilombo cha nyanga ziwiri ngati mwana wa nkhosa (chomwe ndi ulamuliro wamphamvu kwambiri padziko lonse wa Britain ndi America, womwenso ndi mutu wa 7 wa chilombo choyambirira chija) n’chimene chinalimbikitsa anthu kuti apange chifaniziro cha chilombo ndipo chinapereka moyo kwa chifanizirocho.—Chivumbulutso 13:1, 11, 14, 15.
9 Komanso, ena mwa mayiko omwe anali m’bungwe la League of Nations kuwonjezera pa dziko la Great Britain, ankalamulira m’madera omwe kale ankapanga ina mwa mitu ya chilombo chija, monga Greece (Girisi), Iran (Perisiya), ndi Italy (Roma). Patapita nthawi, maboma amene ankalamulira m’madera omwe kale ankalamulidwa ndi maulamuliro 6 amphamvu kwambiri padziko lonse analowa m’bungweli, lomwe ndi chifaniziro cha chilombo, n’kuyamba kugwirizana nalo kwambiri. Apanso tinganene kuti chilombo chofiira kwambiri chija chinatuluka mwa maulamuliro 7 amphamvu kwambiri padziko lonse.
10. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti chilombo chofiira kwambirichi “n’chimenenso chili mfumu ya 8”? (b) Kodi mtsogoleri wa dziko lomwe linali Soviet Union anasonyeza bwanji kuti akugwirizana ndi bungwe la United Nations?
10 Onani kuti chilombo chofiira kwambirichi “n’chimenenso chili mfumu ya 8.” Izi zikutanthauza kuti bungwe la United Nations masiku ano analipanga kuti lizigwira ntchito ngati boma lapadziko lonse. Ndipo nthawi zina bungweli lachitapo zinthu ngati boma. Mwachitsanzo, bungweli linatumiza asilikali m’madera osiyanasiyana kuti akakhazikitse mtendere, monga ku Korea, kudera la Sinai, m’mayiko ena a ku Africa kuno, ndiponso ku Lebanon. Koma bungweli langokhala chifaniziro chabe cha mfumu. Mofanana ndi chifaniziro chachipembedzo, palokha bungweli lilibe mphamvu. Mphamvu zimene lili nazo zimachokera kwa anthu amene analiyambitsa ndiponso amene amalilambira. Nthawi zina, chifaniziro cha chilombochi chimaoneka chofooka, komabe sichinayambe chasiyidwiratu ndi mayiko olamulidwa ndi atsogoleri ankhanza ngati mmene zinachitikira ndi bungwe la League of Nations, zomwe zinachititsa kuti bungwelo ligwere kuphompho. (Chivumbulutso 17:8) Mu 1987 mtsogoleri wotchuka wa dziko lomwe kale linali Soviet Union anagwirizana ndi apapa a ku Roma polankhula zinthu zogwirizana ndi bungwe la UN. Iye anachita zimenezi ngakhale kuti pa nkhani zina sankagwirizana ndi apapawa ngakhale pang’ono. Iye analimbikitsa mayiko kuti akhazikitse “dongosolo latsatanetsatane lokhazikitsira bata padziko lonse” mothandizidwa ndi bungwe la UN. Mogwirizana ndi mawu otsatira amene mngelo uja anauza Yohane, nthawi idzafika pamene bungwe la UN lidzayamba kuchita zinthu mosonyeza kuti lili ndi mphamvu zambiri. Kenako bungweli nalonso ‘lidzapita ku chiwonongeko.’
Mafumu 10 Adzalamulira kwa Ola Limodzi
11. Kodi mngelo wa Yehova ananena zotani zokhudza nyanga 10 za chilombo chophiphiritsa chofiira kwambiri chija?
11 M’chaputala 16 cha buku la Chivumbulutso, taona kuti mngelo wa 6 ndi wa 7 anakhuthula mbale za mkwiyo wa Mulungu. M’chaputalachi, taphunzira zoti mafumu a padziko lapansi akusonkhanitsidwira ku nkhondo ya Mulungu ya Aramagedo, komanso zoti ‘Mulungu adzakumbukira Babulo Wamkulu.’ (Chivumbulutso 16:1, 14, 19) Tsopano tiphunzira mwatsatanetsatane mmene Mulungu adzaperekere ziweruzo zake pa mafumu a padziko lapansi ndi pa Babulo Wamkulu. Taonani mawu otsatirawa amene mngelo wa Yehova anauza Yohane. Mngeloyo anati: “Nyanga 10 zimene unaona zija, zikuimira mafumu 10 amene sanalandirebe ufumu wawo. Koma adzalandira ulamuliro monga mafumu ndipo adzalamulira limodzi ndi chilombo kwa ola limodzi. Mafumuwa maganizo awo ndi amodzi, choncho adzapereka mphamvu zawo ndi ulamuliro wawo kwa chilombocho. Iwowa adzamenyana ndi Mwanawankhosa, koma pakuti iye ndiye Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, Mwanawankhosayo adzawagonjetsa. Komanso oitanidwa aja, amene ali osankhidwa mwapadera ndi okhulupirika, nawonso adzagonjetsa naye limodzi.”—Chivumbulutso 17:12-14.
12. (a) Kodi nyanga 10 zikuimira chiyani? (b) Kodi mfundo yakuti nyanga 10 zophiphiritsa ‘zinali zisanalandirebe ufumu’ ikutanthauza chiyani? (c) Kodi nyanga 10 zophiphiritsa zalandira bwanji “ufumu” panopo, ndipo zilamulira kwa nthawi yaitali bwanji?
12 Nyanga 10 zikuimira maboma onse andale amene panopa akulamulira padzikoli, amenenso amagwirizana ndi chifaniziro cha chilombo. Masiku ano pali mayiko ochepa kwambiri amene ankadziwika m’nthawi ya Yohane. Ndipo mayiko omwe analipo, monga Iguputo (Egypt) ndi Perisiya (Iran), ali ndi dongosolo loyendetsera boma losiyana kwambiri ndi limene anali nalo pa nthawiyo. Choncho, m’nthawi ya Yohane, ‘nyanga 10 zinali zisanalandirebe ufumu wawo.’ Koma panopa m’tsiku la Ambuye, nyangazi zili ndi “ufumu,” kapena kuti ulamuliro wandale. Ndipo mphamvu za maufumu akuluakulu omwe ankalamulira mayiko ena zitatha, makamaka kuyambira pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, mayiko ambiri atsopano anakhazikitsidwa. Mayiko amenewa, pamodzi ndi mayiko omwe anakhazikitsidwa kalekale, ayenera kulamulira ndi chilombo kwa kanthawi kochepa, kapena kuti “kwa ola limodzi.” Kenako Yehova adzathetsa dongosolo lonse la maulamuliro andaleli pa Aramagedo.
13. Kodi mawu akuti nyanga 10 zili ndi ‘maganizo amodzi’ akutanthauza chiyani, ndipo zimenezi zimachititsa kuti nyangazi zizimuona bwanji Mwanawankhosa?
13 Masiku ano, mtima wokonda kwambiri dziko lawo, ndi chimodzi mwa zinthu zamphamvu kwambiri zomwe zikulimbikitsa nyanga 10 zimenezi. Mawu akuti “maganizo awo ndi amodzi,” akutanthauza kuti iwo amafunitsitsa kuteteza ufulu wawo woti akhale mayiko odzilamulira okha m’malo movomereza Ufumu wa Mulungu. Chimenechi chinali cholinga chachikulu chimene chinawachititsa kuti poyamba alowe m’bungwe la League of Nations komanso la United Nations. Iwo ankafuna kukhazikitsa mtendere padziko lonse kuti mayiko awo akhalepobe. Mtima umenewu ukutsimikizira kuti nyanga zija zimatsutsana ndi Mwanawankhosa, yemwe ndi “Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu.” Izi zili choncho chifukwa Yehova anakonza zoti Ufumu wake, womwe wolamulira wake ndi Yesu Khristu, posachedwapa uchotse maufumu onsewa n’kuyamba kulamulira.—Danieli 7:13, 14; Mateyu 24:30; 25:31-33, 46.
14. Kodi zikutheka bwanji kuti olamulira a dzikoli achite nkhondo ndi Mwanawankhosa, ndipo zotsatira zake zidzakhala zotani?
14 Komabe, palibe chimene olamulira a dzikoli angachite polimbana ndi Yesu weniweniyo. Iye ali kumwamba, kutali kwambiri moti iwo sangafikeko. Koma abale a Yesu, a mbewu ya mkazi omwe adakali padziko lapansi, amaoneka kuti ndi osatetezeka. (Chivumbulutso 12:17) Zambiri mwa nyanga zija zasonyeza kale kuti zimadana ndi abale a Yesu amenewa, ndipo pochita zimenezi nyangazi zakhala zikumenyana ndi Mwanawankhosa. (Mateyu 25:40, 45) Koma posachedwapa, nthawi ikwana yoti Ufumu wa Mulungu ‘uphwanye ndi kuthetsa maufumu ena onsewo.’ (Danieli 2:44) Pa nthawi imeneyo, mafumu a padzikoli adzamenyana ndi Mwanawankhosa pa nkhondo yawafawafa, monga momwe tionere kutsogoloku. (Chivumbulutso 19:11-21) Koma panopa tikutha kuona kuti mitundu ya anthu sidzapambana. Ngakhale kuti maboma a anthuwa komanso bungwe la UN, lomwe likuimiridwa ndi chilombo chofiira kwambiri, ali ndi ‘maganizo amodzi,’ sangagonjetse “Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu.” Iwo sangagonjetsenso “oitanidwa aja, amene ali osankhidwa mwapadera ndi okhulupirika,” omwe akuphatikizapo otsatira a Yesu odzozedwa omwe adakali padziko lapansi pano. Amenewanso adzakhala atapambana pa nkhondo chifukwa chotumikirabe Mulungu ndi mtima wosagawanika poyankha mabodza amene Satana wakhala akuwanamizira.—Aroma 8:37-39; Chivumbulutso 12:10, 11.
Kusakaza Hule Lija
15. Kodi mngelo uja ananena zotani zokhudza hule lija, nanga anafotokoza kuti nyanga 10 ndi chilombo chija zidzaliona bwanji huleli ndipo zidzalichita zinthu zotani?
15 Nyanga 10 zija sikuti zimangodana ndi anthu a Mulungu okha. Mngelo uja tsopano anauza Yohane zinthu zina zokhudza hule lija. Yohane anati: “Kenako mngeloyo anandiuza kuti: ‘Madzi amene wawaona aja, pamene hule lija lakhala, akuimira mitundu ya anthu, makamu, mayiko, ndi zinenero. Nyanga 10 waziona zija, komanso chilombo, zimenezi zidzadana nalo hulelo. Zidzalisakaza ndi kulisiya lamaliseche. Zidzadya minofu yake ndi kulinyeketsa ndi moto.’”—Chivumbulutso 17:15, 16.
16. N’chifukwa chiyani Babulo Wamkulu sadzatha kudalira madzi ake kuti amuteteze akadzaukiridwa ndi maboma andale?
16 Mofanana ndi Babulo wakale yemwe ankadalira madzi ochuluka a m’mitsinje yake monga chitetezo, Babulo Wamkulu masiku ano amadalira anthu ake ambirimbiri ochokera mu “mitundu ya anthu, makamu, mayiko, ndi zinenero.” Moyenerera, mngeloyu akutiuza kaye zimenezi asanatiuze za zinthu zoopsa zomwe zidzachitike, zoti maboma andale a padzikoli adzaukira Babulo Wamkulu ndi kumusakaza. Ndiyeno kodi anthu amenewo, ochokera mu “mitundu ya anthu, makamu, mayiko, ndi zinenero,” adzachita chiyani? Anthu a Mulungu ayamba kale kuchenjeza Babulo Wamkulu kuti madzi ake a mumtsinje wa Firate adzauma. (Chivumbulutso 16:12) Pamapeto pake madzi onsewo adzatheratu moti sadzathanso kuthandiza hule lakale la makhalidwe onyansali m’njira iliyonse pa nthawi yomwe lidzafunikire kwambiri thandizo.—Yesaya 44:27; Yeremiya 50:38; 51:36, 37.
17. (a) N’chifukwa chiyani chuma chimene Babulo Wamkulu ali nacho sichidzamupulumutsa? (b) N’chifukwa chiyani mapeto a Babulo Wamkulu adzakhale ochititsa manyazi kwambiri? (c) Kuwonjezera pa nyanga 10, kapena kuti mayiko osiyanasiyana, kodi n’chiyaninso chidzasakaze nawo Babulo Wamkulu?
17 Apa zikuonekeratu kuti chuma chambirimbiri chimene Babulo Wamkulu ali nacho sichidzamupulumutsa. Mwinanso chidzachititsa kuti Babulo Wamkulu ameneyu awonongedwe mofulumira. Izi zili choncho chifukwa masomphenyawa akusonyeza kuti chilombo ndi nyanga 10 zidzamuukira mwankhanza n’kumuvula mkanjo wake wachifumu ndiponso zinthu zake zodzikongoletsera. Chotero zidzamulanda chuma chake. Komanso zidzavula huleli ndi “kulisiya lamaliseche,” kusonyeza kuti khalidwe lake loipa lidzaonekera poyera. Zoonadi, huleli lidzasakazidwa koopsa. Komanso lidzatha mochititsa manyazi kwambiri. Chilombo ndi nyanga 10 zija zidzaliwononga, ndipo “zidzadya minofu yake” n’kungolisiya mafupa okhaokha. Pamapeto pake ‘zidzalinyeketsa ndi moto.’ Huleli lidzatenthedwa ndi moto ngati kuti lafa ndi mliri woopsa ndipo silidzaikidwa n’komwe m’manda. Sikuti ndi mayiko okha, omwe akuimiridwa ndi nyanga 10, amene adzawononge huleli. Nachonso “chilombo,” chomwe chikuimira bungwe la UN, chidzagwirizana ndi nyangazo polisakaza. Bungweli lidzalamula mayiko kuti awononge zipembedzo zonyenga. Ndipo ambiri mwa mayiko oposa 190 omwe ali m’bungwe la UN, asonyeza kale kuti amadana ndi zipembedzo, makamaka Matchalitchi Achikhristu. Zimenezi zaonekera bwino ndi mmene akhala akuvotera pa nkhani zosiyanasiyana m’bungweli.
18. (a) Kodi ndi zinthu ziti zomwe zasonyeza kale kuti maboma akhoza kutembenukira zipembedzo zachibabulo? (b) Kodi n’chiyani chidzachititse kuti Babulo Wamkulu aukiridwe komaliza?
18 N’chifukwa chiyani mayiko adzachitire nkhanza zoterezi mkazi yemwe ankachita naye zachiwerewereyu? Posachedwapa, zomwe zakhala zikuchitika m’mayiko osiyanasiyana zikusonyeza kuti maboma akhoza kutembenukira zipembedzo zachibabulo. Malamulo a boma opondereza zipembedzo achepetsa kwambiri mphamvu zimene zipembedzo zinali nazo m’mayiko monga China ndiponso mayiko omwe kale anali dziko la Soviet Union. M’mayiko omwe muli zipembedzo zambiri zachipulotesitanti ku Ulaya, anthu ambiri alibenso chidwi ndi chipembedzo ndipo ena amakayikira ziphunzitso zake. Zimenezi zachititsa kuti m’matchalitchi muzikhala mopanda anthu, moti tinganene kuti chipembedzo chaferatu m’mayikowa. Komanso anthu a m’chipembedzo cha Katolika, chomwe n’chachikulu kwambiri, akugalukira tchalitchichi ndipo chagawanika. Atsogoleri achipembedzochi akulephera kuthetsa mavuto amenewa. Komabe, tisaiwale kuti kuukiridwa komaliza kwa Babulo Wamkulu kumeneku kudzachitika monga chiweruzo cha Mulungu pa huleli, chomwe sichingasinthe.
Adzachita Mogwirizana ndi Maganizo a Mulungu
19. (a) Kodi chiweruzo chimene Yehova anapereka mu 607 B.C.E. ku mzinda wa Yerusalemu womwe unali wampatuko, chikuchitira bwanji chithunzi chiweruzo chimene adzapereke kwa hule lalikulu lija? (b) Popeza mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa mu 607 B.C.E. unasanduka bwinja ndipo palibe munthu yemwe ankakhalamo, kodi zimenezi zikusonyeza kuti n’chiyani chichitike m’nthawi yathu ino?
19 Kodi Yehova adzapereka chiweruzo chake m’njira yotani? Zimene Yehova anachitira anthu akale ampatuko zikuchitira chithunzi zimene zidzachitike. Ponena za anthu amenewa, iye anati: “Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndaona zinthu zoopsa. Iwo achita chigololo ndi kuchita zinthu mwachinyengo. Alimbikitsa anthu ochita zoipa kuti aliyense asafooke ndi kusiya kuchita zoipa zake. Kwa ine, onsewo akhala ngati Sodomu ndipo anthu okhala mumzindawu akhala ngati Gomora.” (Yeremiya 23:14) Mu 607 B.C.E., Yehova anagwiritsa ntchito Nebukadinezara kuti ‘avule zovala’ za mzinda womwe unkachita chigololo chauzimuwo, ndi ‘kutenga zinthu zake zokongola ndi kuusiya wosavala ndi wamaliseche.’ (Ezekieli 23:4, 26, 29) Matchalitchi Achikhristu masiku ano amachita zinthu zofanana ndi zimene Yerusalemu wa pa nthawiyo ankachita. Ndipo mogwirizana ndi zimene Yohane anaona m’masomphenya a m’mbuyomu, Yehova adzapereka chilango ngati chimenechi kwa Matchalitchi Achikhristu ndiponso kwa zipembedzo zina zonse zonyenga. Mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa mu 607 B.C.E., unasanduka bwinja ndipo simunkakhala anthu. Zimenezi zikusonyeza mmene Matchalitchi Achikhristu adzakhalire akadzalandidwa chuma chake n’kuchititsidwa manyazi. Ndipo zipembedzo zina zonse zonyenga, zomwenso ndi mbali ya Babulo Wamkulu, nazonso zidzawonongedwa.
20. (a) Kodi Yohane anasonyeza bwanji kuti Yehova adzagwiritsanso ntchito anthu olamulira popereka chiweruzo chake? (b) Kodi “maganizo” a Mulungu ndi otani? (c) Kodi mayiko adzachita bwanji zinthu ndi “maganizo awo amodzi,” koma kodi kwenikweni iwo adzakhala akuchita zinthu zogwirizana ndi maganizo a ndani?
20 Yehova adzagwiritsanso ntchito anthu olamulira kuti apereke chiweruzo chake. Mngelo uja anapitiriza kuuza Yohane kuti: “Pakuti Mulungu anaika izi m’mitima yawo kuti zichite monga mwa maganizo ake, kuti zikwaniritse maganizo awo amodzi, mwa kupereka ufumu wawo kwa chilombo, kufikira mawu a Mulungu atakwaniritsidwa.” (Chivumbulutso 17:17) Kodi “maganizo” a Mulungu ndi otani? Maganizo ake ndi akuti asonkhanitse pamodzi anthu oti aphe Babulo Wamkulu n’cholinga chomusakaziratu. Komabe, olamulira adzaukira Babulo Wamkulu ameneyu pofuna kuchita zinthu zogwirizana ndi “maganizo awo amodzi.” Iwo adzaukira hule lalikululi poganiza kuti akuchita zinthu zokomera mayiko awo. Mwina atsogoleriwa adzayamba kuona kuti zipembedzo zimene zili m’mayiko awo zikhoza kuukira ulamuliro wawo. Koma iwo adzachita zimenezi chifukwa Yehova ndi yemwe adzakhale akuyendetsa zinthu. Atsogoleriwa adzachita zinthu zogwirizana ndi maganizo ake ndipo kamodzi n’kamodzi, adzawononga mdani wa Mulungu wakalekale yemwenso ndi wachigololo.—Yerekezerani ndi Yeremiya 7:8-11, 34.
21. Popeza Mulungu adzagwiritsa ntchito chilombo chofiira kwambiri powononga Babulo Wamkulu, kodi zikuoneka kuti mayiko adzachita chiyani ndi bungwe la United Nations?
21 Zoonadi, mayiko adzagwiritsa ntchito chilombo chofiira kwambiri, chomwe chikuimira bungwe la United Nations, powononga Babulo Wamkulu. Koma iwo sadzachita zimenezi mwa kufuna kwawo chifukwa Yehova adzaika maganizo ake m’mitima yawo ‘kuti achite monga mwa maganizo ake, kuti akwaniritse maganizo awo amodzi, mwa kupereka ufumu wawo kwa chilombo.’ Nthawi imeneyi ikadzakwana, zikuoneka kuti mayiko adzaona kuti akufunika kulimbitsa bungwe la United Nations. Iwo adzakhala ngati apereka mano ku bungweli, kutanthauza kuti adzalipatsa udindo ndi mphamvu zawo zonse kuti liukire zipembedzo zonyenga n’kuzigonjetsa “kufikira mawu a Mulungu atakwaniritsidwa.” Choncho, hule lakalekaleli lidzawonongedwa ndipo silidzakhalaponso.
22. (a) Kodi mawu omaliza a mngelo uja a pa Chivumbulutso 17:18, akusonyeza chiyani? (b) Kodi Mboni za Yehova zikuchita chiyani pamene zadziwa tanthauzo la chinsinsi chimene Yohane anauzidwa?
22 Potsimikizira mfundo yakuti Yehova adzaweruza zipembedzo zonyenga zonse pamodzi, mngelo uja anamaliza ndi mawu akuti: “Ndipo mkazi amene unamuonayo akuimira mzinda waukulu umene ukulamulira mafumu a dziko lapansi.” (Chivumbulutso 17:18) Mofanana ndi Babulo wa m’nthawi ya Belisazara, Babulo Wamkulu ‘wayezedwa pasikelo ndipo wapezeka kuti akuperewera.’ (Danieli 5:27) Iye adzaphedwa mofulumira kwambiri ndipo sadzakhalaponso. Nanga kodi anthu a Mboni za Yehova akuchita chiyani pamene adziwa tanthauzo la chinsinsi chokhudza hule lalikulu ndiponso chilombo chofiira kwambiri? Iwo akulengeza mwachangu za tsiku la Yehova lopereka chiweruzo, ndipo akamagwira ntchitoyi, amayankha ‘mwachisomo’ anthu omwe akufunafuna choonadi moona mtima. (Akolose 4:5, 6; Chivumbulutso 17:3, 7) Monga mmene tionere m’mutu wotsatira, onse amene akufuna kupulumuka pamene hule lalikulu lija likuwonongedwa, ayenera kuchitapo kanthu mwamsanga.
[Zithunzi patsamba 252]
Maulamuliro 7 Amphamvu Kwambiri Padziko Lonse Omwe Alamulira Motsatizanatsatizana
IGUPUTO
ASURI
BABULO
MEDIYA NDI PERISIYA
GIRISI
ROMA
BRITAIN NDI AMERICA
[Zithunzi patsamba 254]
“N’chimenenso chili mfumu ya 8”
[Chithunzi patsamba 255]
Iwo sakufuna n’komwe kuyang’ana Mwanawankhosa, ndipo ‘akupereka mphamvu zawo ndi ulamuliro wawo kwa chilombo’
[Chithunzi patsamba 257]
Matchalitchi Achikhristu, omwe ndi mbali yaikulu ya Babulo Wamkulu, adzawonongedwa n’kukhala bwinja ngati Yerusalemu wakale