Nsautso ya Maganizo Pamene Yakantha Mkristu
AKATSWIRI a umoyo wa maganizo amanena kuti mwinamwake munthu mmodzi mwa 5 mu United States amavutika ndi mkhalidwe wina wozindikirika wa kusalongosoka kwa maganizo. World Health Organization yawonjezera kuti pangakhale mamiliyoni ochuluka kufika ku 40 a matenda a maganizo osachiritsidwa m’maiko otukuka kumene. Mavuto a maganizo akhoza ngakhale kupezeka pakati pa nzika za zisumbu za uparadaiso za Pacific.
Chotero sichiyenera kutidabwitsa kuti chiŵerengero cha Akristu lerolino chikukumana ndi mavuto a maganizo kapena a malingaliro kuchokera ku kudera nkhaŵa kopepuka ndi kupsyinjika kwakung’ono kufika ku matenda owopsya onga ngati kupsyinjika kwakukulu, kusemphana kwa mphamvu ya minyewa (kupsyinjika koipa), mantha, ndi kusokonezeka kwa maganizo. Ena anali ndi mavuto oterowo asankhale Mboni, pamene ena ayamba kuvutika ndi nsautso yoteroyo m’zaka zawo za uchikulire.
Chifukwa Chimene Akristu Saliri Otetezeredwa
Mkazi Wachikristu wina wa zaka zoposa pa 20 za utumiki wodzipereka anasimba kukhala atasautsidwa ndi mawu okakamiza ndi owumirira. “Ndidzakhala ndikulingalira pa nkhani ina iriyonse,” anatero mkaziyo, “ndipo panabwera liwu lonena kuti, ‘dziphe.’. . . Mobwerezabwereza umamva mawu amenewa kufikira sukhoza kupirira nazo mpang’ono pomwe.” Kodi chiri chothekera motani kwa Mkristu wokhulupirika kuvutika mwanjira yotere? Kodi 2 Timoteo 1:7 samanena kuti: “Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha, komatu wamphamvu ndi chikondi ndi [kulongosoka kwa maganizo, NW]”?
Inde, koma kulongosoka kwa maganizo mwachisawawa kumalozera mochepera ku kukhala bwino kwa malingaliro kuposa ku kuthekera kwa kuchita kwa Mkristu ndi chiweruzo chozikidwa m’Baibulo. Mosiyana ndi munthu wa kudziko yemwe ali “mumdima mwa maganizo,” kapena “wovunditsitsa maganizo,” Mkristu ‘watembenuza maganizo ake’ mwa kuphunzira Mawu a Mulungu. (Aefeso 4:17, 18; 2 Timoteo 3:8; Aroma 12:2) Ichi mosakaikira chimachita zambiri kuchirikiza kukhazikika kwa malingaliro ndi maganizo a Mkristu, komabe sichimampanga iye kukhala wotetezeredwa ku mavuto a umoyo wa maganizo. Atumiki ena okhulupirika a Mulungu mu nthaŵi za Baibulo, onga ngati Epafrodito, anavutika ndi mitundu ya nsautso ya maganizo.—Afilipi 2:25, 26; Luka 2:48.
“Mwa Adamu onse amafa,” mtumwi Paulo amatikumbutsa tero. (1 Akorinto 15:22) Ambiri a ife tiri ndi kulemala kowonekera kwa kuthupi. Ena amavutika ndi matenda a maganizo kapena malingaliro.
Zochititsa Nsautso ya Maganizo
Nsonga za kuthupi zimawonekera kukhala muzu wa nkhani zambiri za nsautso ya maganizo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za munthu amene maso ake “amawona zachilendo.” Zochititsa za kuwona zideruderu kozizwitsa koteroko? “Kuchedwa pali winyo”! (Miyambo 23:29-33) Mwachiwonekere, zakumwa zoledzeretsa zingapangitse ubongo kuwona zideruderu. Adokotala amanena kuti mwanjira yofananayo, tsatanetsatane wa ubongo wokhala ndi vuto, nsonga zobadwa nazo m’mitsempha, ndipo mothekera ngakhale kadyedwe kangapangitse ubongo kusagwira ntchito bwino. Mavuto a maganizo ndi a malingaliro angatulukepo.a
Kudidikiza kwamphamvu kwa maganizo, konga ngati kupsyinjika, kungayambitsenso mavuto a malingaliro. Kokha kungoyesera kusungirira makhalidwe oyera ndi umunthu Wachikristu “m’nthawi zovuta kuchita nazo” zino kungakhale magwero a kupsyinjika. (2 Timoteo 3:1-5) Nkulekelanji, popeza kuti ngakhale Loti “anadzizunzira moyo wake wolungama” pa kuipa kumene iye anawunikiridwako tsiku ndi tsiku mu Sodomu! (2 Petro 2:8) Ndiponso, Akristu ena ayambukiridwa mwamanganizo chifukwa cha kugwiriridwa chigololo, kuipitsidwa mwa kugonana, kapena chifukwa cha makhalidwe apapitapo a zochita zosakhala za lamulo kapena kugwiritsira ntchito molakwa anangoneka. Zinthu zoterozo zingadzetse chiŵerengero chodzetsa mantha pa umoyo wa maganizo wa munthu.
Chimene Akulu Angachite
Akulu ali odera nkhaŵa ndi kuweta nkhosa zonse zoikidwa m’chisamaliro chawo—kuphatikizapo awo ovutika ndi nsautso ya malingaliro. (1 Petro 5:2; Yesaya 32:1, 2 ) Zowona, iwo sali adokotala, ndipo sangachiritse anthu matenda awo kuposa mmene mtumwi Paulo anachiritsira Epafrodito matenda ake akuthupi kapena kupsyinjika kotsatirapo. (Afilipi 2:25-29) Komabe, mwa kusonyeza kurdera nkhaŵa kwenikweni ndi kudzimva kwaumunthu, iwo kaŵirikaŵiri angachite zochulukira kuthandiza ndi kulimbikitsa oterewa.—1 Petro 3:8.
Bwanji, kenaka, ngati mbale ayamba kuchita mwachilendo kapena kudandaula za kusinthasintha kwa malingaliro? Akulu choyamba angayesere kukokera wodwalayo, kuyesera kugamulapo kokha chomwe chikumuvuta iye. Kodi tsoka laumwini kapena mkhalidwe wachilendo wotsendereza—mwinamwake kutaikiridwa kwa ntchito kapena imfa ya wokondedwa—zampangitsa iye kukhala “wosalinganizika kwa kanthaŵi kochepa? (Mlaliki 7:7) Kodi wokanthidwayo ali wopsyinjika mwapang’ono chifukwa cha kusungulumwa ndipo chotero ali m’kusowa kwa winawake “wolankhula motonthoza” kwa iye? (1 Atesalonika 5:14) Kapena chingakhale kuti mbaleyo ali wovutitsidwa chifukwa cha zophophonya zaumwini? Kutsimikiziridwa kwa chikondi cha Mulungu ndi chifundo—limodzi ndi uphungu woyenera—kungathandize kuchotsa kudera nkhaŵa kwake. (Salmo 103:3, 8-14) Ubwino woposa ungakwaniritsidwe kokha mwa kupemphera ndi mbale wosautsidwayo.—Yakobo 5:14.
Akulu angagawanenso nzeru zogwira ntchito ndi wovutikayo. (Miyambo 2:7) Mwachitsanzo, tadziŵitsa kuti kusokonezeka kwina kwa malingaliro kungakhale kogwirizana ndi kadyedwe. Akulu chotero angapereke malingaliro akuti mbale adye chakudya cholinganizika ndi kupewa kadyedwe konkitsa. Kapena iwo angazindikire kuti munthu wosautsidwayo wakhala pansi pa chitsenderezo chokulira pa ntchito yake ndipo angakhoze kupindula mokulira kuchokera ku “mpumulo wokulira”— mokhazikika kwenikweni kupeza tulo tabwino tausiku.—Mlaliki 4:6.
Awo ‘Ofuna Sing’anga’
Ngati nsautso yoipa ipitirizabe, ngakhale ndi tero, chiri chabwino kukumbukira mwau a Yesu: “Olimba safuna sing’anga ayi, koma odwala.” (Mateyu 9:12) Anthu osautsidwa ambiri amakhala osinkhasinkha kuwonana ndi sing’anga. Akulu ndi ziwalo za banja chotero angafunikire kulimbikitsa mbaleyo kufunafuna chisamaliro cha mankhwala, monga ngati kufufuzidwa kotheratu ndi dokotala wokhulupiriridwa, Profesa Maurice J. Martin akunena kuti: “Unyinji wosiyanasiyana wa matenda a kuthupi umangolingaliridwa kukhala kusokonezeka kwa maganizo.” Ndipo ngakhale kumene matenda amaganizo ndithudi ali olowetsedwamo, mankhwala okhutiritsa kaŵirikaŵiri amakhalapo.
Mkazi wa mkulu akunena mmene mwamuna wake wosokenezeka “anakhala ndi mantha kukhala pafupi ndi abale ndipo sanafune kupita ku misonkhano. . . . Iye mosowa chochita anafuna kufa!” Koma pambuyo pa kulandira chisamaliro cha mankhwala chaluso, mkhazi wake anali wopkhoza kusimba kuti: “Iye salinso wopsyinjika mozama, ndipo samafunanso kukhala kunja kwa misonkhano. M’mawa muno iye wapereka nkhani ya poyera!”
Movomerezeka, si mikhalidwe yonse yomwe imathetsedwa mopepuka chotere. Sayansi ikungoyamba kumene kuthetsa zozizwitsa za mavuto a maganizo. Kufufuzidwa molongosoka ndi kupatsidwa mankhwala kungakhale njira yaitali, yovuta kwenikweni—koma kaŵirikaŵiri imathandiza.
Okanthidwa ndi Ziwanda?
Minkhole ina ya kuvutika kwa maganizo imawopa kuti iri pansi pa kuwukiridwa ndi ziwanda, akumadzinenera nthaŵi zina kukhala akumva “mawu.” Zowona, ziwanda zadziŵika kupangitsa anthu openga kuchita mosokonezeka. (Marko 5:2-6, 15) Palibe chitsimikiziro chakuti ziwanda ziri zolowetsedwamo m’milandu yambiri ya mkhalidwe wosokonezeka, monga mmene ziliri zakuti izo ziri zolowetsedwa m’milandu yonse ya kusalankhula, khungu, ndi khunyu. Komabe, kumbuyo mu nthaŵi za Baibulo, ziwanda nthaŵi zina zingapangitsa (kapena chifupifupi kukulitsa) matenda amenewa! (Mateyu 9:32, 33; 12:22, 17:15-18) Baibulo limapanga kusiyanitsa kowonekera bwino, ngakhale ndi tero, pakati pa “odwala ndi okhala ndi ziwanda.” (Marko 1:32-34; Mateyu 4:24; Machitidwe 5:16) Motsimikizirika, kenaka, unyinji wokulira wa milandu ya khungu kapena khunyu lerolino imachititsidwa ndi nsonga za kuthupi—osati nsonga za—uchiwanda. Zofananazo mosakaikira zinganenedwe za milandu yambiri ya nsautso ya maganizo.
Komabe, chiyenera kukumbukiridwa kuti Satana ndi ziwanda zake ‘akumenya nkhondo’ ndi anthu a Mulungu ndipo adziŵika kukhala akuvutitsa Akristu okhulupirika. (Chivumbulutso 12:17; Aefeso 6:12) Ziwanda ziri zoipa, ndipo sichiyenera kutidabwitsa kuti zimatenga chisangalalo chokulira m’kuzunza miyoyo ina yosautsidwa m’maganizo—ikumakulitsa zovuta zawo.
Chotero ngati akulu ali ndi zifukwa zabwino za kukaikira kuti chiyambukiro cha uchiwanda chikuphatikizidwa, palibe kuvulaza kulikonse m’kupanga kwawo kufufuza kwina. Kodi munthuyo, mwachitsnzo, analandira zinthu zokaikiritsa mwachindunji ndipo mwadala kuchokera kwa anthu omwe ali olowetsedwa mu mkhalidwe winawake wa uchiwanda? Kutaya zinthu zoterozo kungabweretse mpumulo. (Machitidwe 19:18-20) Popeza kuti Akristu akuwuzidwa “kutsutsa Mdyerekezi,” akulu anagalangizenso wokanthidwayo kukana “mawu” aliwonse achilendo omwe angakhale achiyambi cha uchiwanda. (Yakobo 4:7; Mateyu 4:10) Ngati munthu akudzimva kukhala pansi pa kuwukiridwa, iye ayenera kupemphera mokhazikika, kuitana pa dzina la Yehova mofuula.—Aefeso 6:18; Miyambo 18:10.
Kulowetsedwa kwa uchiwanda, ngakhale ndi tero, kumawonekera kukhala kopatulidwa—osati kolamulira. Mlongo wina akulongosola kuti: “Ndinalingalira kuti ndinali ndi chiwanda kufikira ndinafunafuna thandizo la mankhwala ndipo ndinadziŵitsidwa kuti ndinali ndi tsatanetsatane wina wosakhazikika. Chinandipatsa ine mpumulo waukulu kupeza kuti anali matenda omwe anapangitsa machitidwe anga ndipo osati munthu wina wauchiwanda yemwe anali mkati mwanga!”
Mankhwala a Maganizo
Mankhwala osiyanasiyana tsopano akugwiritsiridwa ntchito ndi adokotala m’kuchiritsa kusokonezeka kwa maganizo. Kugwiritsiridwa ntchito koyang’aniridwa kwa mankhwala oterowo kwalola Akristu odwala moipitsitsa kugwira ntchito mwachibadwa. Abale ena okhala ndi zolinga zabwino, ngakhale ndi tero, akhumudwitsa odwala kutenga mankhwala olembedwa, mwinamwake akumawopa kuti angakhale ovulaza kapena omwerekeretsa. Pali, ndithudi, ngozi zophatikizidwa ndi mtundu uliwonse wa kupatsidwa mankhwwala, ndipo “wochenjera asamalira mayendedwe ake,” akumalingalira zotulukapo za nthaŵi yaitali.—Miyambo 14:15.
Mosangalatsa, ngakhale kuli tero, anamgoneka a maganizo ambiri sali okhoza kuwonetsa zideruderu, kupereka mpumulo, kapena kumwerekeretsa; amatumikira kokha kulungamitsa tsatanetsatane wosakhazikika mu ubongo. Mankhwala olinganizidwa kuchiritsa kusokomezeka, mwachitsanzo, angathandize kuchepetsako kusokonezeka kwa kaŵirikaŵiri kwa zizindikiro za kusokonezeka kwa maganizo. Lithium ingathandize kuchepetsako kupsyinjika ndi kuthetsa zachilendo za kupsyinjika koipa.
Chitayerekezedwa, anamgoneka amphamvu nthaŵi zina amagwiritsiridwa ntchito kupereka mpumulo kwa wodwala kapena kudidikiza zizoloŵezi za kudzipha. Komabe, ngati mbale akutenga mankhwala olembedwa osati kaamba ka zosangalatsa koma kuti agwire ntchito mwachibadwa, ichi chingawonedwe m’njira yofananayo monga munthu wodwala matenda a shuga wogwiritsira ntchito insulin.
Chiyenera kukumbukiridwa kuti mankhwala a amaganizo kaŵirikaŵiri amagwira ntchito pang’onopang’ono ndipo angakhale ndi ziyambukiro zosasangalatsa. Nthaŵi zina, kachiŵirinso, pali mlingo wa kuyesera ndi kuphonya kwa adokotala m’kupeza mankhwala ogwira ntchito ndipo/kapena unyinji wa mankhwala womwe ungatulutse ziyambukiro zapambali zochepa koposa. Odwala kaŵirikaŵiri amakhumudwitsidwa. Ziwalo za banja ndi ena chotero angakhale ochirikiza kwa munthu wotenga mankhwalayo, kumulimbikitsa iye kukhala woleza mtima ndi kugwirizana ndi anthu oyeneretsedwa a za mankhwala. Bwanji ngati iye ali ndi mafunso ponena za mankhwala ena? Kapena bwanji ngati mavuto abuka kapena mankhwala awonekera kukhala osagwira ntchito? Mavuto oterowo ayenera kukambitsiridwa ndi dokotala wake.b Ngati kuli koyenera, lingaliro lachiŵiri lingatengedwe.
Kuchiritsa kwa Kulankhula
M’nkhani zina, kulingalira kungaperekedwenso kukhala ndi wodwala akulankhula nkhanizo ndi munthu wophunzitsidwa bwino. Mwinamwake dokotala wa banja wokhulupiriridwa yemwe ali wozolowerana mwaumwini ndi wodwalayo angatumikire mwanjirayi. Bwanji, ngakhale ndi tero, ponena za kulandira kupatsidwa mankhwala kuchokera kwa dokotala wa maganizo kapena katswiri wodziŵa zamalingaliro? Ichi chingakhale chosankha chaumwini choyenera kupangidwa ndi chenjezo. Akatswiri a njira zochiritsira amasiyanasiyana m’kufikira kwawo kwa kuchiritsa. Ena, mwachitsanzo, amachita kachitidwe ka kufufuza malingaliro ka Freud. kutsimikizirika kwake kumene kumatokosedwa ndi ambiri m’munda wa umoyo wa za maganizo.
Chodetsa nkhaŵa kwenikweni chiri nsonga yakuti ochita ena okhala ndi zolinga zabwino apatsa malingaliro omwe amatsutsana mwachindunji ndi Baibulo. Kulephera kumvetsetsa maprinsipulo Achikristu—ngakhale kuwona oterowo kukhala “kupusa”—akatswiri a njira zochiritsira ena akhoza ngakhale kutsiriza kuti kutsatira lamulo la makhalidwe abwino osamalitsa a Baibulo kuli magwero a mavuto a munthuyo!—1 Akorinto 2:14.
Ngakhale kuli tero, asing’anga ena, kuphatikizapo akatswiri a za malingaliro ndi adokotala a maganizo, amapereka mitundu ina ya kuchiritsa kwa kulankhula yomwe siiri kwenikweni kusanthula kwa malingaliro koma iri njira zothandizira wodwalayo kumvetsetsa matenda ake, kuchirikiza kufunika kwa mankhwala, ndi kuthetsa mavuto ogwira ntchito. Mkristu angapeze kupatsidwa mankhwala koteroko kukhala kothandiza, koma afunikira kulungamitsa nsonga zake asanalandire kupatsidwa mankhwalako: Kokha kodi nchiyani chimene kupatsidwa mankhwalako kumaphatikiza? Kodi ndi uphungu wotani womwe udzaperekedwa? Kodi sing’angayo amamvetsetsa ndi kuyamikira zikhulupiriro za Mboni za Yehova?c Ngati kuchiritsa kwa kulankhula kwavomerezedwa, ‘yesani mawu’ a dokotala m’malo mongolandira chirichonse mosakaikira.—Yobu 12:11, 12.
Kwa mbali yaikulu, kenaka, nsautso ya maganizo ingawonedwe kukhala vuto la mankhwala—osati lauzimu. Kumvetsetsa nsonga imeneyi, mabanja, akulu, ndi ziwalo za mpingo zingakhale zochirikiza bwino lomwe kwa ovutikawo. Panthaŵi zina osautsidwawo amafunikiranso kuchirikiza kwauzimu. Mmene mpingo ungaperekere ichi chidzalingaliridwda m’kope lamtsogolo.
[Mawu a M’munsi]
a Onani makope a October 22, 1987, Chingelezi, ndi July 8, 1987, a magazini yathu inzake, Galamukani!
b Sosaite simayamikira kapena kupereka chiweruzo pa mankhwala osiyanasiyana ndi kupatsidwa mankhwala kogwiritsiridwa ntchito ndi adokotala. Kufufuza m’zofalitsidwa za Sosaite kungakhoze, ngakhale ndi tero, kutsimikizira kukhala kwa thandizo.
c Ngati wodwalayo ali ndi vuto la kulongosola kaimidwe kake kozikidwa pa Baibulo kwa sing’anga kapena katswiri wa njira zochiritsira, mwinamwake Mkristu wachikulire wina angamthandize iye.
[Chithunzi patsamba 26]
Mwa kukhala omvetsera otonthoza ndi aphungu, akulu kaŵirikaŵiri angathandize anthu odwala nsautso ya malingaliro
[Chithunzi patsamba 29]
Nthaŵi zina chiri cholangizidwa kaamba ka munthu wodwala maganizo kufunafuna thandizo la mankhwala