Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • “Mwina Tsopano Asintha”
    Galamukani!—2001 | November 8
    • “Mwina Tsopano Asintha”

      ROXANAa ndi mayi wansangala ndiponso wokongola, wa ana anayi ndipo mwamuna wake ndi dokotala wotchuka pa ntchito yake ya opaleshoni ku South America. Iye anati, “Akazi amaona kuti mwamuna wanga ndi munthu wosangalatsa zedi, ndipo amuna nawo amam’konda kwambiri.” Koma mwamuna wa Roxana ali ndi vuto limene ngakhale anzake apamtima salidziŵa. “Akakhala kunyumba ankasanduka chilombo choopsa. Ndi wansanje kwambiri.”

      Pamene akupitiriza nkhani yake, Roxana akuonekeratu kuti ali ndi nkhaŵa. “Vutoli linayamba titakwatirana kwa milungu yochepa chabe. Azichimwene anga ndi amayi anga anabwera kudzatichezera ndipo ndinasangalala ndiponso kuseka nawo kwambiri. Koma atachoka, mwamuna wanga anandikankha mwamphamvu n’kundigwetsera pa sofa, atakalipa kwambiri. Sindinathe kumvetsa kuti akuchitiranji zimenezi.”

      N’zomvetsa chisoni kuti uku kunali kuyamba chabe kwa mavuto a Roxana, chifukwa wakhala akumenyedwa molapitsa kwa zaka zambiri tsopano. Roxana amadziŵiratu zimene mwamunayo anazoloŵera kuchita akam’menya. Amati akam’menya, amamupepesa kwambiri ndipo amalonjeza kuti sadzachitanso. Akatero amasintha khalidweli kwa kanthaŵi. Kenaka amayambiranso kuchita zoopsazi. Roxana anati, “Ndimangoti mwina tsopano asintha. Ngakhale ndikam’thaŵira, nthaŵi zonse ndimabwereranso.”

      Roxana amaopa kuti tsiku lina khalidwe la mwamuna wakeli lidzafika poipa. Iye anati, “Anandiopsezapo kuti adzandipha, adzapha ana athu ndipo kenaka adzadzipha yekha. Tsiku lina anandipana pakhosi ndi sizasi. Tsiku linanso anandiopseza ndi mfuti, anailozetsa pa khutu panga, n’kuikhetchemula! Mwayi wake inalibe zipolopolo, koma pang’onong’ono n’kanafa ndi mantha.”

      Ambiri Saulula

      Monga Roxana, akazi ambiri padziko lonse akuvutitsidwa ndi amuna omenya.b Ambiri saulula zimenezi ayi. Amaganiza kuti kuwaneneza amuna awo si kungathandize n’komwe. Ndiponsotu amuna ambiri savomera zakuti amamenyadi akazi awo ponena kuti “Mkazi wanga amaganiza mothamanga” kapena kuti “Mkaziyu amakonda kuwonjezera nkhani.”

      N’zomvetsa chisoni kuti panyumba pawo penipeni, akazi ambiri amakhala mtima uli m’mwamba poopa kumenyedwa, m’malo moti azikhala mosatekeseka. Koma n’zodandaulitsa kuti nthaŵi zambiri anthu amamvera chisoni omenya mnzakeyo m’malo mwa omenyedwayo. N’zoonadi, anthu ena sakhulupirira n’komwe kuti munthu wooneka ngati waulemu wake angamenye mkazi wake. Taganizirani zimene anakumana nazo mkazi wina dzina lake Anita pamene anaulula kuti mwamuna wake waulemu wake ndithu anali kum’menya. “Mnzathu wina anandiuza kuti: ‘N’zoona iwe ungam’nenere zoipa zotere mwamuna wabwino ngati ameneyu?’ Mnzathu winanso ananena kuti mwina ineyo ndinali kum’puta dala! Ndipo ngakhale pamene mwamuna wangayu anadziŵikadi khalidwe lake, anzanga ena anayamba kundithaŵa. Akuti bwenzi nditangopirira chifukwa chakuti paja ‘amuna ndi achoncho.’”

      Zimene anaona Anitazi zikusonyeza kuti ambiri zimawavuta kumvetsa mmene zimapwetekera ukamamenyedwa ndi mwamuna wako. Kodi n’chiyani chimachititsa mwamuna kuchitira mkazi amene amati amamukonda nkhanza zotere? Kodi omenyedwawo angathandizidwe bwanji?

  • Kodi Amuna Amamenyeranji Akazi?
    Galamukani!—2001 | November 8
    • Kodi Amuna Amamenyeranji Akazi?

      AKATSWIRI ena amati akazi amene amaphedwa ndi amuna awo n’ngochuluka kuposa amene amaphedwa ndi anthu ena onse. Poyesa kuthetsa vuto la kumenya akazi, akatswiri ambiri akhala akufufuza nkhaniyi. Kodi ndi mwamuna wotani amene amamenya mkazi wake? Kodi ubwana wake unali wotani? Kodi ali pachibwenzi analinso munthu wovuta? Kodi mwamuna womenyayo amatani anthu ena akamam’thandiza maganizo?

      Chinthu chimodzi chimene akatswiriŵa atulukira n’chakuti si kuti amuna omenya akazi awo n’ngofanana zochitika. Pali ena amene amamenya akazi awo mwakamodzikamodzi. Sagwiritsa ntchito zida ndipo alibe chizoloŵezi chomenya akazi awo. Amuna otereŵa sanyanyuka mtima nthaŵi zonse ndipo amaoneka kuti chilipo chinthu china chimene chimawachititsa kutero. Ndiye pali amuna ena amene anazoloŵera kumenya akazi awo. Amawamenya nthaŵi zonse ndipo siziwakhudza n’komwe akatero.

      Koma ngakhale kuti pali amuna omenya akazi awo mosiyanasiyana si ndiye kuti pali kumenya kwabwinoko. Inde, khalidwe lililonse lomenya mkazi lingathe kum’vulaza mwinanso kumupha ndithu. Motero ngakhale kuti wina amamenya mkazi wake mwa apo ndi apo kapena amangom’menya pang’ono poyerekezera ndi ena si ndiye kuti alibe mlandu. Kunena zoona palibe kumenya mkazi “kovomerezeka.” Koma kodi ndi zinthu zotani zimene zingachititse mwamuna kumenya mkazi amene iye yemwe analumbira kuti adzam’konda kwa moyo wake wonse?

      Kutsanzira Makolo

      N’zosadabwitsa kuti amuna ambiri omenya akazi awo nawonso anakulira m’mabanja otero. “Amuna ambiri omenya akazi awo anakulira m’mabanja okhalira ‘nkhondo,’” analemba choncho Michael Groetsch, amene kwa zaka makumi aŵiri wakhala akufufuza nkhani ya kumenya akazi. “Pamene anali makanda ndiponso ana, amuna ameneŵa ankakhala m’makomo mmene kupweteketsana mitima ndiponso kumenyana zinkachitika ‘monga khalidwe la nthaŵi zonse.’” Katswiri wina anati, mwamuna amene anakula akuona khalidwe lotere “angatengere adakali mwana khalidwe la abambo ake loona akazi ngati achabechabe. Mnyamatayo amaphunzira kuti nthaŵi zonse mwamuna ayenera kulamulira akazi ndipo kuti njira yake ndiyo kuwaopseza, kuwapweteketsa mtima, ndi kuwanyoza. Komanso amaphunzira kuti njira yabwino yosangalatsira abambo ake ndiyo kutsanzira zimene iwo amachita.”

      Baibulo limalongosola momveka bwino kuti khalidwe la kholo lingathe kukhudzanso mwana kwambiri, m’njira yabwino kapena yoipa. (Miyambo 22:6; Akolose 3:21) N’zoona kuti ngakhale mwamuna anakulira m’banja lomenyana si ndiye kuti m’pomveka akamamenya mkazi wake, koma zimangopereka umboni wakuti nkhanza zakezo anazitengera m’banja la kwawo.

      Kuvuta Chifukwa cha Chikhalidwe

      M’madera ena amati kumenya mkazi si nkhani ayi, amangoti ndiko kukhala. “M’madera ambiri anthu amakhulupirira kuti mwamuna ali ndi ufulu womenya kapena kuopseza mkazi wake,” linatero lipoti la bungwe la United Nations.

      Ngakhale m’madera amene khalidweli n’losaloleka, anthu ambiri amamenya akazi awo. Amuna ena amawaganizira zoopsa kwambiri akazi awo. Malingana ndi nyuzipepala ya ku South Africa ya Weekly Mail and Guardian, atafufuza ku Cape Peninsula anapeza kuti amuna ambiri amene ankati savuta akazi awo ankaganiza kuti kumenya mkazi si nkhani ndipo ankati ukamenya mkazi si ndiye kuti ukumuvuta.

      Zikuoneka kuti nthaŵi zambiri anthu amayamba kuganiza molakwa chonchi adakali ana. Mwachitsanzo ku Britain, atafufuza anapeza kuti anyamata 75 pa 100 alionse a zaka 11 ndi 12 amaona kuti mwamuna ali ndi ufulu womenya mkazi wake ngati atamuyamba.

      Palibe Chifukwa Chokwanira Chomenyera Mkazi

      Mfundo zili pamwambazi zingathandize kudziŵa chifukwa chimene amuna amamenyera akazi, koma si zikutanthauza kuti ayenera kutero. Kunena mosapita m’mbali, kumenya mkazi ndi tchimo lalikulu kwambiri pamaso pa Mulungu. M’Mawu ake, Baibulo, timaŵerenga kuti: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha; pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Kristu Eklesia.”—Aefeso 5:28, 29.

      Baibulo linalonjeza kale kuti mu “masiku otsiriza” a nthaŵi ino, anthu ambiri adzakhala “ovutitsa,” “opanda chikondi chachibadwa,” ndiponso “aukali.” (2 Timoteo 3:1-3; The New English Bible) Kuchuluka kwa amuna ovutitsa akazi awo n’chizindikiro china chongosonyeza kuti tikukhala m’nthaŵi yeniyeni yotchulidwa mu ulosiwu. Koma kodi akazi amene amamenyedwa ndi amuna awo n’kuwathandiza bwanji? Kodi zingatheke n’komwe kuti amuna omenya akazi awo asinthe khalidweli?

      [Mawu Otsindika patsamba 5]

      “Mwamuna womenya mkazi wake ndi wolakwa mofanana ndi munthu womenya munthu amene sakum’dziŵa.”—Linatero buku lakuti, When Men Batter Women

      [Bokosi patsamba 6]

      Kudzitukumula Chifukwa Chokhala Mwamuna Ndi Vuto la Padziko Lonse

      Padziko lonse, pali anthu ena amene ali ndi kamtima kodzitukumula poti ndi amuna ndipo motero amavutitsa akazi awo. Lipoti lotsatirali likusonyeza zimenezi.

      Egypt: Atafufuza kwa miyezi itatu ku Alexandria anapeza kuti akazi ambiri amavulala makamaka chifukwa chomenyedwa ndi amuna awo. Motero kumeneko akazi 100 alionse amene amapita kuchipatala cha anthu ovulala, opitirira 27 amakhala atamenyedwa. Inatero ndemanga ina yachidule yachisanu pa msonkhano wa Fourth World Conference on Women.

      Thailand: M’dera lalikulu kwambiri la kunja kwa mzinda wa Bangkok, theka la akazi okwatiwa amamenyedwa kaŵirikaŵiri. Linatero bungwe la Pacific Institute for Women’s Health.

      Hong Kong: “Akazi amene akuti akhala akumenyedwa ndi amuna awo awonjezereka modabwitsa n’kufika 40 pa 100 alionse m’chaka chathachi,” inatero nyuzipepala ya South China Morning Post, ya pa July 21, 2000.

      Japan: Akazi ofunafuna kokhala pothaŵa kuzunzidwa analipo 4,843 mu 1995 koma anachuluka n’kufika pa 6,340 mu 1998. “Pafupifupi mkazi mmodzi pa akazi atatu alionse pa gululi anali kufunafuna kokhala chifukwa chomenyedwa ndi mwamuna wake,” inatero nyuzipepala ya Japan Times, ya pa September 10, 2000.

      Britain: “M’dziko lonse la Britain pa masekondi sikisi alionse kunyumba kwinakwake munthu wina amakhala akugwiriridwa, kumenyedwa kapena kubayidwa.” Malingana ndi lipoti la apolisi ofufuza milandu mwachinsinsi a ku Britain otchedwa Scotland Yard, akuti “apolisi amalandira matelefoni 1,300 kuchokera kwa anthu ovutitsidwa panyumba tsiku lililonse, kutanthauza kuti pachaka apolisiŵa amalandira matelefoni oposa 570,000. Anthu 81 pa 100 alionse ochitidwa zimenezi amakhala akazi ovutitsidwa ndi amuna,” inatero nyuzipepala yotchedwa The Times, ya pa October 25, 2000.

      Peru: Milandu 70 mwa milandu 100 iliyonse imene imapita ku polisi n’njokhudza akazi omenyedwa ndi amuna awo. Linatero bungwe la Pacific Institute for Women’s Health.

      Russia: “M’chaka chimodzi chokha, akazi 14,500 a ku Russia anaphedwa ndi amuna awo, ndipo enanso 56,400 analemazidwa kapena kuvulazidwa kwambiri pomenyedwa ku nyumba zawo,” inatero nyuzipepala ya The Guardian.

      China: “Ndi vuto la posachedwa. Likumka lichuluka, makamaka m’madera a m’tauni,” anatero pulofesa Chen Yiyun, mkulu wa bungwe la Jinglun Family Center. “Masiku ano anthu saopa kuti oyandikana nawo angadziŵe akamamenyana m’nyumba mwawo, inatero nyuzipepala ya Guardian.

      Nicaragua: “Ku Nicaragua khalidwe lomenya akazi likuchuluka. Ofufuza ena anati chaka chatha chokha akazi oposa theka la akazi onse a ku Nicaragua anavutitsidwapo ndi amuna awo.” Izi zinali nkhani zoulutsidwa pa wailesi ya BBC.

      [Bokosi patsamba 7]

      Zimene Zingasonyeze Kuti Mwina Mwamuna Ndi Womenya

      Ofufuza amene anatsogoleredwa ndi Richard J. Gelles wa pa yunivesite yotchedwa Rhode Island, ku United States, anapeza kuti izi ndizo zinthu zimene zingasonyeze kuti mwina mwamuna ali ndi khalidwe lomenya ndiponso lozunguza mkazi m’banja:

      1. Ngati kale mwamunayo anavutitsapo mkazi wake.

      2. Ngati sali pantchito.

      3. Ngati amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo ngakhale kamodzi kokha pa chaka.

      4. Ngati kunyumba kwawo ankaona bambo ake akumenya amayi ake.

      5. Ngati anthuwo si okwatirana; anangoloŵana.

      6. Akamalandira ndalama zochepa ngati ali pa ntchito.

      7. Ngati sanaphunzire mokwanira.

      8. Ngati ali ndi zaka zoyambira 18 mpaka 30.

      9. Ngati kholo lake limodzi kapena onse ankakonda kumenya ana kunyumba kwawo.

      10. Ngati ali osauka kwambiri.

      11. Ngati mwamuna ndi mkaziyo ali osiyana chikhalidwe.

      [Chithunzi patsamba 7]

      Kumenyana pa khomo kungawononge kwambiri khalidwe la ana

  • Kuthandiza Akazi Omenyedwa ndi Amuna Awo
    Galamukani!—2001 | November 8
    • Kuthandiza Akazi Omenyedwa ndi Amuna Awo

      KODI akazi amene amamenyedwa ndi amuna awo angathandizidwe bwanji? Choyamba, muyenera kumvetsetsa mavuto amene akukumana nawo. Nthaŵi zambiri amuna otere si kuti amangowamenya chabe akaziwo. Amawaopsezanso ndi kuwanyoza motero amangodziona ngati ndi achabechabe.

      Tatiyeni tione nkhani ya Roxana imene taisimba m’nkhani yoyamba ija. Nthaŵi zina mwamuna wake amam’nyoza mopweteketsa mtima kwambiri. Roxana anaulula mavuto ake motere: “Amanditchula mayina ondinyoza. Amandiuza kuti: ‘Mbuli iwe, sunamalize n’komwe sukulu. Ungathe bwanji kusamala ana popanda ine? Ndiwe mayi waulesi ndiponso wosathandiza. Ukuganiza kuti ngakhale aboma angakulole kusamalira anaŵa popanda ineyo?’”

      Mwamuna wa Roxana amasunga ndalama zonse kuti mkazi wake asakhale ndi mphamvu zilizonse. Sam’lola kuyendetsa galimoto yawo, ndipo tsiku lililonse sipatenga nthaŵi asanaimbe telefoni kuti adziŵe zimene mkazi wake akuchita. Akati anenepo maganizo ake pa nkhani inayake, mwamunayo amayamba kukalipa moopsa. Motero Roxana amadziŵiratu kuti sayenera kunenapo maganizo ake pa nkhani iliyonse.

      Apatu tingathe kuona kuti nkhani ya kuvutitsa mkazi ndi yovuta. Kuti mum’thandize mkaziyo muyenera kumvetsera mokhudzidwa mtima. Musaiwale kuti nthaŵi zambiri zimawavuta kwambiri akazi kulongosola zimene zakhala zikuwachitikira. Cholinga chanu chikhale cholimbikitsa mkaziyo pamene akuthana pang’onopang’ono ndi vutolo.

      Akazi ena omenyedwa angafune kupempha chithandizo ku boma. Nthaŵi zina kuchita chinthu china chachikulu, monga kupita ku polisi, kungachititse mwamuna womenya kudziŵa kuti imeneyi si nkhani yamaseŵera ayi. Koma n’zoona kuti nkhaniyo ikangotha basi maganizo onse osiya khalidweli amaiwalika.

      Kodi mkazi womenyedwayo ayenera kum’siya mwamunayo? Baibulo silinena kuti nkhani ya kupatukana n’njaing’ono. Komanso silikakamiza mkazi womenyedwa ndi mwamuna wake kukhalabe ndi mwamunayo amene angathe kudzam’vulaza kwambiri mwinanso kumupha kumene. Mtumwi wachikristu Paulo analemba kuti: ‘Ngati am’siya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo.’ (1 Akorinto 7:10-16) Chifukwa chakuti Baibulo sililetsa kupatukana ngati pali vuto lalikulu kwambiri, zimene mkazi angaganize kuchita pankhaniyi munthu wina sangam’pangire. (Agalatiya 6:5) Munthu wina aliyense sayenera kum’nyengerera kuti asiye mwamuna wake, komanso sayenera kum’kakamiza kuti akhalebe ndi mwamunayo ngati akuopera kuti avulala kapena kufa kapenanso kuti am’sokoneza pa zauzimu.

      Kodi Amuna Omenya Akazi Awo Angasinthe?

      Kuvutitsa mkazi n’kuphwanya poyera mfundo za chikhalidwe za m’Baibulo. Pa Aefeso 4:29, 31, timaŵerenga kuti: “Nkhani yonse yovunda isatuluke mkamwa mwanu . . . Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.”

      Mwamuna aliyense amene amatsatira Yesu sanganene kuti amakonda mkazi wake ngati amam’zunza. Ngati mwamuna amazunza mkazi wake, ndiye kuti zabwino zonse zimene mwamunayo amachita zili n’ntchito yanji? Munthu ‘wandewu’ si woyenera maudindo apadera mumpingo wachikristu. (1 Timoteo 3:3; 1 Akorinto 13:1-3) Inde, aliyense wodzitcha Mkristu amene amachita zinthu mopsa mtima kaŵirikaŵiri komanso wosalapa angathe kuchotsedwa mumpingo wachikristu.—Agalatiya 5:19-21; 2 Yohane 9, 10.

      Kodi amuna andewu angathe kusintha khalidwe? Ena asintha. Komabe nthaŵi zambiri amuna omenya akazi awo samasintha pokhapokha (1) ngati atavomereza kuti khalidwe lawolo n’loipa, (2) ngati akufunadi kuleka khalidwe lawolo, ndiponso (3) ngati akufunafuna kuthandizidwa. Mboni za Yehova zapeza kuti Baibulo ndilo lingathe kum’sintha kwambiri munthu. Anthu ambiri achidwi amene amaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ayamba kufunitsitsa kumusangalatsa Mulungu. Anthu ongoyamba kumene kuphunzira Baibulo ameneŵa amaphunzira kuti Yehova Mulungu ‘amada aliyense wokonda chiwawa.’ (Salmo 11:5) N’zoona kuti mwamuna womenya ayenera kusinthanso zinthu zina osangosiya kumenya kokhako. Mwamunayo amafunika kuti aphunzirenso kuona mkazi wake m’njira yosiyana kwambiri.

      Mwamuna akadziŵa Mulungu, amaphunzira kuona mkazi wake monga “wom’thangatira” osati monga wantchito kapena wonyozeka koma monga woyenera kumupatsa “ulemu.” (Genesis 2:18; 1 Petro 3:7) Amaphunziranso kukhala wachifundo ndiponso kumvetsera maganizo a mkazi wake. (Genesis 21:12; Mlaliki 4:1) Ntchito yophunzitsa anthu Baibulo imene Mboni za Yehova zimachita yathandiza mabanja ambiri. M’banja lachikristu si muyenera kupezeka munthu wankhanza kapena womenya anzake.—Aefeso 5:25, 28, 29.

      “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.” (Ahebri 4:12) Motero, nzeru zopezeka m’Baibulo zingathandize mabanja kuona bwino mavuto awo ndi kuwalimbitsa mtima kuti athane ndi mavutowo. Chofunikanso kwambiri n’chakuti m’Baibulo muli chiyembekezo chotsimikizika ndiponso cholimbitsa mtima chakuti m’dzikoli simudzakhalanso kuzunzana Mfumu yakumwamba yosankhidwa ndi Yehova ikamadzalamulira anthu onse omvera. Baibulo limati: “Adzapulumutsa waumphaŵi wopfuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. Adzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.”—Salmo 72:12, 14.

      [Mawu Otsindika patsamba 12]

      M’banja lachikristu si muyenera kupezeka munthu wankhanza kapena womenya anzake

      [Bokosi patsamba 8]

      Kukonza Mabodza

      • Akazi amene amamenyedwa amawayamba dala amuna awo.

      Amuna ambiri savomera mlandu womenya akazi awo chifukwa amati akaziwo amachita kuwaputa dala. Nthaŵi zina ngakhale anzawo abanjalo angavomereze kuti n’zoonadi mkaziyo ndi wovuta, ndipo mpake kuti nthaŵi zambiri mwamuna wake amalephera kupirira. Komatu kutero kumakhala kulungamitsa wolakwayo n’kuimba mlandu womenyedwayo. Kunena zoona, akazi omenyedwa amayesetsa kwambiri kuziziritsa mtima amuna awo. Komatu palibiretu chifukwa chilichonse chokwanira kuti munthu amenye mkazi wake. Buku lina lonena za khalidwe la amuna omenya lotchedwa The Batterer—A psychological Profile limati: “Amuna amene mabwalo amilandu amawalamula kuti akalangidwe chifukwa chovutitsa akazi awo amakhala kuti anazoloŵera kwambiri kuchita za ndewu. Amachita zimenezi pofuna kuphwetsa ukali ndi kukhazikitsa maganizo, kusonyeza mphamvu ndi kuthetsa nkhani, komanso pofuna kuziziritsa mtima. . . . Nthaŵi zambiri sangathe kuvomereza kuti ali ndi vuto kapena siziwakhudza n’komwe zoti ali ndi vutoli.”

      • Moŵa umachititsa kuti munthu azimenya mkazi wake.

      Inde, n’zoona kuti amuna ena amakhala andewu kwambiri akamwa moŵa. Koma kodi n’kwanzeru kunena kuti moŵawo ndi umene umawachititsa zimenezi? “Munthu womenya mkazi wake ataledzera amapeza ponamizira, m’malo movomera kuti iyeyo ndiye ali ndi khalidwe loipa,” analemba choncho, K. J. Wilson m’buku lake lakuti When Violence Begins at Home. Iye anapitiriza kunena kuti: “Zikuoneka kuti kwa anthufe, ambiri timaona kuti ngati mwamuna wamenya mkazi wake ataledzera m’pomveka. Mkazi womenyedwayo safuna kuvomereza kuti mwamuna wake ndi wovuta, koma amangoti ndi chidakwa.” Wilson anati maganizo otere, angapusitse mkaziyo n’kumayembekeza kuti “ngati mwamunayo atangosiya kumwa moŵa, basi sadzam’menyanso.”

      Pakali pano, ofufuza ambiri amaona kuti vuto la uchidakwa ndi kumenya mkazi ndi mavuto aŵiri osiyana. Ndiponsotu amuna ambiri omwa mwauchidakwa kapena amene amagwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo samenya akazi awo. Anthu amene analemba buku lakuti When Men Batter Women anaona kuti: “Chimapangitsa amuna kusasiya kumenya akazi awo n’chakuti kumenyako kumatheketsa kuti azilamulira akaziwo, kuwaopseza ndiponso kuwagonjetsa. . . . Amuna otere amakhala kale ndi khalidwe lauchidakwa ndiponso logwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Koma n’kulakwa kuganiza kuti moŵa kapena mankhwala osokoneza bongo n’zimene zimawapangitsa kukhala andewu.”

      • Amuna omenya akazi awo amachitira nkhanza munthu aliyense.

      Nthaŵi zambiri munthu womenya mkazi wake amatha kukhala munthu wabwino kwambiri kwa ena. Iye amasinthasintha zochita kukhala ngati birimankhwe. Ichi n’chifukwa chake anzawo a banjalo sakhulupirira akamauzidwa kuti mwamunayo n’ngwa ndewu. Koma zoona zake zimakhala zakuti mwamunayo amakhala chilombo kwa mkazi wake.

      • Akazi sadandaula n’kuzunzidwa.

      N’kutheka kuti anthu amaganiza zimenezi chifukwa chosamvetsa kuti mkazi womenyedwa amalephera kuthaŵa chifukwa chosoŵa kothaŵira. Mkazi womenyedwayo angathe kukhala ndi anzake amene angam’sunge mwina kwa mlungu umodzi kapena iŵiri, koma akachoka pakhomopo kodi angatani payekha? Amatheratu mphamvu akamaganiza kuti ayenera kupeza ntchito ndiponso kulipira nyumba ya lendi kwinakunso akusamalira ana. Ndipo malamulo a m’dzikolo angam’letse kuthaŵa nawo anawo. Ena anathaŵapo koma amuna awo anawafunafuna n’kuwapeza kenaka n’kubwerera nawo kunyumba, mowakakamiza kapena mowanyengerera. Anzawo amene sangamvetse kuti chachitika n’chiyani angaganize molakwa kuti akazi otere sadandaula n’kuzunzidwa.

  • “Nthaŵi Zina Ndimangoona Ngati N’kutulo Ndithu!”
    Galamukani!—2001 | November 8
    • “Nthaŵi Zina Ndimangoona Ngati N’kutulo Ndithu!”

      Lourdes akusuzumira pa windo ali m’nyumba yake n’kumayang’ana mzindawo ndipo wagwira pakamwa pake pamene pakunjenjemera ndi mantha. Iyeyu ndi mayi wa ku Latin-America amene anavutitsidwa kwambiri ndi mwamuna wake womenya Alfredo kwa zaka zoposa 20. Chinachake chinam’chititsa Alfredo kusintha khalidwe lakelo. Koma panopa zimam’vutabe kwambiri Lourdes kuti alongosole mmene anazunzidwira.

      Ndi mawu ofooka, Lourdes anasimba motere: “Vutoli linayamba titangokwatirana kwa masabata aŵiri. Nthaŵi ina anandimenya n’kundichotsa mano aŵiri. Nthaŵi inanso ataponya nkhonya yake ndinazinda ndipo anamenya kabati ya zovala. Koma chinkandipweteka kwambiri chinali kumanditchula mayina ondinyoza. Ankanditcha ‘chitsiru chosatha ntchito’ ndipo ankangonditenga ngati wosaganiza bwino. Ndinkafuna kuchoka, koma kodi ana atatu n’kanaloŵera nawo kuti?”

      Alfredo akusisita pheŵa la Lourdes mwachikondi. Iye akuti: “Ndili ndi udindo waukulu kuntchito kwanga ndipo ndinachita manyazi nditapatsidwa chisamani komanso chikalata cha ku boma chondiletsa kumenya mkazi wanga. Ndinayesetsa kusintha, koma pasanathe nthaŵi ndinayambiranso.”

      Nanga zinthu zinasintha bwanji? Lourdes amene tsopano akuoneka kuti wakhazikika maganizo akulongosola motere: “Mkazi wa pa sitolo ina yake ali m’gulu la Mboni za Yehova ndipo anandiuza kuti n’tafuna angathe kundithandiza kumvetsa Baibulo. Ndinaphunzira kuti Yehova amaŵerengera akazi kuti ndi ofunika. Ndinayamba kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova, ngakhale kuti poyamba Alfredo zinkam’psetsa mtima kwambiri. Nditapita ku Nyumba ya Ufumu kanali koyamba kuti ndichezeko ndi anzanga. Ndinadabwa kuona kuti ndinali ndi ufulu wokhala ndi chikhulupiriro changachanga, chimene ndikanatha kuuza ena mwaufulu. Ndinazindikira kuti Mulungu amandiona kuti ndine wofunika. Zimenezi zinandilimbitsa mtima.

      “Pali chinthu chimodzi chachikulu chimene sindidzaiŵala. Alfredo anali kupitabe ku Misa yachikatolika Lamlungu lililonse, ndipo ankadana nazo zimene ndinali kuchita ndi Mboni za Yehova. Ndinamuyang’anitsitsa n’kunena mwachifatse koma molimba mtima kuti: ‘Alfredo, maganizo ako ndi osiyana ndi anga.’ Ndipo sanandimenye! Pasanapite nthaŵi yaitali ndinabatizidwa ndipo kuyambira nthaŵi imeneyo patha zaka zisanu asanandimenye.”

      Koma apa anali atangoyamba chabe kusintha. Alfredo analongosola kuti: “Patatha zaka zitatu Lourdes atabatizidwa, mnzanga wina wa m’gulu la Mboni za Yehova anandiitana kunyumba kwake, ndipo anandilongosolera zinthu zosangalatsa kwambiri zochokera m’Baibulo. Ndiye ndinayamba kuphunzira naye Baibulo koma mkazi wanga sindinamuuze. Posapita nthaŵi ndinayamba kutsagana naye mkazi wanga Lourdes ku misonkhano. Nkhani zambiri zimene ndinamva kumeneko zinali zokhudza banja, ndipo nthaŵi zambiri ndikamvetsera nkhanizi manyazi ankandigwira kwambiri.”

      Alfredo anagoma kuona anthu amumpingo, ndi amuna omwe, akusesa misonkhano ikatha. Atapita kunyumba zawo, anakaona amuna akuthandiza akazi awo kutsuka mbale. Zinthu zazing’ono ngati zimenezi zinam’thandiza Alfredo kuona mmene chikondi chenicheni chimakhalira.

      Posapita nthaŵi, Alfredo anabatizidwa ndipo panopa iye ndi mkazi wake akuchita ntchito ya utumiki wolalikira wa nthaŵi zonse. Lourdes anati “Nthaŵi zambiri amandithandiza kukonza patebulo tikamaliza kudya ndiponso kuyala pabedi. Amandiyamikira n’kaphika chakudya, ndipo amandilola kusankha zimene ndikufuna, monga nyimbo zimene ndikufuna kumvetsera komanso katundu wa m’nyumba amene tikufuna kugula. Likanakhala kale Alfredo sakanandilola n’komwe kutero! Posachedwapa, kwa nthaŵi yoyamba, anandigulirako maluŵa posonyeza kuti amandikonda. Nthaŵi zina ndimangoona ngati n’kutulo ndithu!”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena