Mutu 2
M’mene Imfa Imayambukirira Zochita za Tsiku ndi Tsiku za Anthu
ANTHU ambiri ali odera nkhawa kwambiri ndi chimene chimayambukira miyoyo yao ndi ija ya mabanja ao pa tsopano lino. Koma owerengeka ali ofunitsitsa kulankhula kapena kuganiza momka patali ponena za imfa.
Zoona, imfa siri chiyembekezo chosangalatsa, koma iri ndi chiyambukiro chotsimikizirika pa zochita za munthu za tsiku ndi tsiku. Kodi ndani wa ife amene sanakhale ndi chisoni ndi lingaliro lalikulu la kutayikiridwa chifukwa cha imfa ya bwenzi lokondedwa kapena wachibale wapamtima? Imfa m’banja ingasinthe mkhalidwe wonse wa moyo wa banja, kuononga kupezedwa kwa ndalama kokhazikika ndi kuchititsa kusukidwa kapena chisoni kwa otsala’wo.
Ngakhale kuli kwakuti ingakhale yosakondweretsa, imfa iri chochitika cha tsiku ndi tsiku chimene inu muyenera kuchilingalira. Simungapitirizebe machitidwe’wo mopanda mapeto. Mawa kungakhale kochedwa kwambiri.
Kodi imene’yi yakuyambukirani motani? Kodi nthawi zina mumaona kukhala wokakamizidwa ndi kufupika kwa nthawi ya moyo kuyesa mwamphamvu kwambiri kupeza zonse zimene mungathe mu iyo? Kapena, kodi mumatenga lingaliro la choikidwiratu, mukumanena kuti, a, zimene ziti zidzakhale zidzakhale?
LINGALIRO LA CHOIKIDWIRATU
Anthu ambiri lero lino amakhulupirira kuti moyo ndi imfa zimalamuliridwa ndi choikidwiratu. Limene’li ndiro lingaliro la Ahindu oposa mamiliyoni 477. Kunena zoona, malingaliro a choikidwiratu ali ofala kweni-kweni. Kodi simunamve anthu akunena kuti, ‘Zinayenera kuchitika basi,’ ‘Nthawi yake inakwana,’ kapena, ‘Iye anapulumuka chifukwa chakuti nambala yake sinatuluke’? Mau otero’wo amanenedwa kawiri-kawiri mogwirizana ndi ngozi. Kodi ngoona? Lingalirani chitsanzo’chi:
M’kati mwa chionetsero cha kuuluka ndi ndenge pa Paris Air Show mu 1973 ndege ya supasoniki TU-144 ya Soviet Union inaphulika, ikumapha ogwiramo ntchito ake. Zigawo zazikulu za ndege’yo zinagwera pa mudzi wa Goussainville, Fransa. Mkazi wina m’menemo anali atangotseka chitseko cha chipinda chogona pamene chidutswa cha ndege yopasuka’yo chinadzamenya khoma lakunja, chikumagwetsa kotheratu chipinda chogona’cho. Iye sanabvulazidwe.
Ena sanapulumuke. Akufa anaphatikizamo zidzukulu zitatu za mkazi wokalamba’yo, koma osati gogo’yo.
Kodi ana amene’wo ndi ena’wo anafa chifukwa chakuti “nambala” yao kapena “nthawi yao inakwana? Kodi ena’wo anapulumuka chifukwa chakuti nthawi yoikidwiratu inali isanakwane kuti afe kufikira Pambuyo pake?
Awo oyankha mafunso amene’wa a kuti “Inde” amakhulupirira kuti palibe chiri chonse chimene munthu ali yense angachite chingaletse imfa ya munthu ngati ‘nthawi yake yakwana.’ Iwo amalingalira kuti, mosasamala kanthu za kusamala kuli konse kochitidwa, iwo sangapewe konse chimene choikidwiratu chikufuna. Limene’li ndi lingaliro lofanana ndi lija la Agriki akale amene analingalira chokidwiratu cha munthu kukhala chikulamuliridwa ndi milungu yachikazi itatu—Clotho, Lachesis ndi Atropos. Clotho anayerekezeredwa kukhala akupota chingwe cha moyo, Lachesis anapima utali wake ndipo Atropos anachidula pamene nthawi inakwana.
Kodi lingaliro la choikidwiratu lotero’lo ndi loyenera? Dzifunseni kuti: Kodi n’chifukwa ninji chiwerengero cha imfa za ngozi chimatsika pamene malamulo a chisungiko amveredwa ndi kuonjezeka pamene anyalanyazidwa? Kodi n’chifukwa ninji unyinji wa imfa za pa mseu ungasonyezedwe kukhala ukuchititsidwa ndi mphwayi za anthu, kuledzera, kulakwa kapena kusamvera malamulo? Kodi n’chifukwa ninji kuli kwakuti m’maiko okhala ndi miyezo yapamwamba kwambiri ya masungidwe a thupi ndi chakudya chabwino anthu amakhala ndi avereji yokulirapo kwambiri ya utali wa moyo koposa m’maiko opanda zinthu zimene’zi? Kodi n’chifukwa ninji osuta fodya ochuluka koposa osasuta fodya amafa ndi kansala ya mapapu? Kodi ndi motani m’mene zonse’zi zikanakhalira zochititsidwa ndi choikidwiratu chopanda nzeru chimene palibe choletsa? M’malo mwake, kodi si zoona kuti pali zifukwa zochititsa zimene zimachitikira anthu?
Ponena za imfa zambiri za ngozi, kodi si nkhani ya kufika chabe kwea munthu pa malo oopsya? Kuti tilongosole mwa fanizo: Mwamuna wina amachoka pa nyumba pake pa nthawi yakuti-yakuti tsiku la ntchito liri lonse. M’mawa wina, pamene akudutsa pa nyumba ya mnansi, iye akumva kupfuula ndi kukalipa iye akuonjezera liwiro la kuyenda kwake ndipo, pamene iye akungokhota pa gulaye, iye akulasidwa ndi chipolopolo chosochera. Imfa yake iri chifukwa cha kukhala pa gulaye’yo pa nthawi yokakwika; mkhalidwe’wo unali wosaonedweratu.
Ataona zimene zimachitika kweni-kweni m’moyo wa tsiku ndi tsiku, wolemba wanzeru wa bukhu la Baibulola Mlaliki anati: “Ndinabwera’nso ndi kuzindikira pansi pano kuti omwe atamanga msanga sapambana m’liwiro, ngakhale olimba sapambana m’nkhondo, ngakhale anzeru sapeza zakudya, ngakhale ozindikira bwino salemera, ngakhale odziwitsa sawakomera mtima; koma yense angoona zom’gwera m’nthawi mwake.”—Mlaliki 9:11.
Munthu amene amazindikira zimene’zi samanyalanyaza malamulo a chisungiko ndi kudziika pa upandu mosafunika, akumalingalira kuti iye ngwosati n’kufikiridwa imfa malinga ngati “nthawi” yake sinakwane. Iye amazindikira kuti lingaliro la choikidwiratu lingakhale laupandu, kwa iye mwini ndi kwa ena’nso. Chidziwitso chimene’chi, chitagwiritsiridwa ntchito mwanzeru, chingaonjezere zaka zochuluka ku moyo wanu.
Ndipo’nso, lingaliro la choikidwiratu lingasogolere ku machitidwe a ukandifere, ndipo lingachititse’nso munthu kukhala wamphwayi ndi kuphunzira zinthu zimene zingayambukire kwambiri iye ndi banja lake.
KUKHALIRA MOYO TSOPANO LOKHA BASI
Kuphatikiza pa lingaliro la choikidwira’tulo, zochitika za m’zaka za zana la makumi awiri zasonkhezera machitidwe a anthu.
Talingalirani kwa kanthawi zimene zachitika. Mamiliyoni ambiri aonongeka monga akufa ndi nkhondo, upandu, ziwawa ndi njala. Mpweya ndi madzi zochirikiza moyo’zo zikuipitsidwa pa liwiro lochititsa mantha. Mwachionekere ku mbali iri yonse moyo wa munthu ukuopsyezedwa. Ndipo palibe chiri chonse choti chipereke chitsimikiziro cheni-cheni chakuti mtundu wa anthu udzakhala wokhoza kuthetsa mabvuto ake posachedwapa m’tsogolo muno. Moyo ukuonekera kukhala wosatsimikizirika kwambiri. Kodi chotulukapo chake n’chiani?
Okhala pa dziko lapansi ambiri akukhalira moyo tsopano lokha, kupeza chiri chonse chothekera m’tsiku la lero. Iwo amaona kukhala okakamizika kutero, akumalingalira kuti moyo umene ali nao tsopano ndiwo moyo wokha umene iwo angayembekezere kukhala nao. Moyenerera Baibulo limalongosola lingaliro lao kuti: “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa timwalira.”—1 Akorinto 15:32, NW.
M’kuyesa-yesa kupewa zeni-zeni zosakondweretsa za moyo, iwo angatembenukire ku zakumwa zoledzeretsa kapena mankhwala oledzeretsa. Ena amayesa kupeza potulukira m’zogwiritsa mwala zao ndi kudera nkhawa ndi kufupika kwa moyo mwa kudzilowetsa m’machitidwe a chisembwere a mitundu yonse—dama, chigololo, kugonana kwa amuna okha-okha ndi kugonana kwa akazi okha-okha. Bukhu lakuti Death and Its Mysteries limati:
“Kukuonekera kuti anthu wamba ambiri lero lino akuyambukiridwa ndi kuopa imfa ya onse imene’yi, pafupi-fupi mosadziwa. Kumene’ku mwina mwake ndi kulongosoledwa kwapang’ono kwa kusokonezeka kwa nthawi zathu, kumene kukusonyezedwa ndi upandu wadala, kusakaza, kugonana kosasankha ndi liwiro loonjezeredwa la moyo. Ngakhale nyimbo ndi zamba zamakono zimaonekera kukhala zikusonyeza kutaya mtima kwa anthu amene sakukhulupirira’nso m’tsogolo mwao mwa iwo eni.”
Kodi n’chiani chimene chakhala chotulukapo cha kukhalira moyo lero lokha konse’ko monga ngati kuti sikungakhale mawa?
Awo okonda kumwa kwambiri ndi uchidakwa angaiwale kwakanthawi zobvuta zao. Koma iwo amataya ulemu wao ndipo, ataledzera, nthawi zina amadzibvulaza okha kapena ena. Ndipo m’mawa mwake iwo amapeza kuti aonjezera mutu waching’alula ku mabvuto amene anali nao kale.
Omwerekera ndi mankhwala oledzeretsa, nawo’nso, amalipira mtengo wapamwamba kwambiri kaamba ka kuyesa-seya kwao kupewa cheni-cheni. Iwo kawiri-kawiri amakhala ndi chibvulazo chosatha chakuthupi ndi cha maganizo. Ndipo, kuti achirikize chizolowezi chao choonongetsa ndalama kwambiri’cho, iwo angapeze kuti akudziluluza mwa kulowa m’kuba kapena uhule.
Bwanji kugonana kosasankha? Kodi kumathandiza kuthetsa bvuto la munthu m’moyo? Mosemphana ndi zimene’zo zipatso zake kawiri-kawiri ndizo nthenda zonyansa zopatsana mwa kugonana, mimba zosafunika, ana apathengo, kutaya mimba, mabanja osweka, nsanje yaikulu, kumenyana ndipo ngakhale mbanda.
Ndithudi, anthu ambiri sanagonjere ku kukhala ndi moyo wachisembwere. Komabe iwo sanapewe chitsenderezo chimene chimachokera m’kuzindikira, modziwa kapena modziwa pang’ono, kuti moyo wao udzatha. Podziwa kuti nthawi iri yochepa, iwo angafune-fune kukhala patsogolo m’dziko mofulumira kwambiri monga momwe kungathekere. Limodzi ndi chotulukapo chotani? Kukhumba kwao chuma chakuthupi kungawasonkhezere kutaya kuona mtima kwao. Monga momwe mwambi wa Baibulo moonadi umalongosolera kuti: “Wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.” (Miyambo 28:20) Koma si zokha’zo.
Nthawi yochuluka kwambiri ndi nyonga zimagwiritsiridwa ntchito m’kutsogola mwa zinthu zakuthupi kwakuti pamakhala nthawi yochepa ya kusangalala ndi banja lanu. Zoona, ana angakhale akupeza zinthu zonse zakuthupi zimene iwo amafuna. Koma kodi iwo akupeza chitsogozo ndi chilangizo zimene iwo akufunikira m’malo mwakuti akhale anyamata ndi atsikana odalirika? Makolo ambiri, pamene akuzindikira kuti nthawi yoonongedwa limodzi ndi ana ao iri yochepa’di, samaona kweni-kweni chifukwa chokhalira ndi nkhawa—kufikira kutakhala kochedwa kwambiri. Inde, n’kopweteka kumva kuti mwana wanu wamwamuna wagwidwa kapena mwana wanu wamkazi wanamwali adzabala mwana wosakhala wa mu ukwati.
Mwa zimene zikuchitika lero lino, kodi sikuli koonekera bwino kuti, mosasamala kanthu za kufupika kwa moyo, anthu ambiri afunikira kuphunzira njira yokhutiritsa kwambiri yokhalira ndi moyo?
Kusapeweka koonekera kwa imfa sikumapangitsa munthu ali yense kutaya malamulo abwino a khalidwe, ndipo’nso sikumachititsa mphwayi yozikidwa pa choikidwiratu mwa anthu onse. Mosemphana ndi zimene’zo, zikwi mazana ochuluka lero lino zikusangalala ndi mkhalidwe wabwino kwambiri wa moyo chifukwa cha kusakhala oyambukiridwa moipa kwambiri ndi chiyembekezo cha imfa.
NJIRA YABWINO KWAMBIRI
Itaonedwa bwino, imfa ingatiphunzitse kanthu kena kopindulitsa. Pamene imfa itenga anthu, tingapindule ndi kusinkha-sinkha kolingalira ponena za m’mene tikukhalira ndi miyoyo yathu ya ife eni. Zaka zokwanira zikwi zitatu zapita’zo woyang’anitsitsa mtundu wa anthu anagogomezera chimene’chi, kuti: “Mbiri yabwino iposa zonunkhira zabwino; ndi tsiku la kumwalira liposa tsiku lakubadwa. Kunka ku nyumba ya maliro kupambana kunka ku nyumba ya madyerero; pakuti kuja’ko ndi matsiriziro a anthu onse; ndi omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo . . . Mtima wa anzeru uli m’nyumba ya maliro; koma mtima wa zitsiru uli m’nyumba ya kuseka.”—Mlaliki 7:1-4.
Baibulo pano silikunena kuti kuchita chisoni n’kwabwino koposa kusangalala. M’malo mwake, likusonyeza nthawi yeni-yeni’yo pamene banja likulira maliro chifukwa cha imfa ya mmodzi wa ziwalo zake. Siri nthawi ya kuiwala oferedwa ndi kupitiriza ndi kuchita kwanu madyerero ndi kusangalala. Pakuti, monga momwe imfa yathetsera zolinganiza ndi zochita zonse za wakufa’yo, ingachite chimodzi-modzi ndi zathu. Munthu amachita bwino kudzifunsa kuti: Kodi ndikuchitanji ndi moyo wanga? Kodi ndikupanga dzina kapena mbiri yabwino? Kodi ndimathandizira motani chimwemwe ndi thanzi la ena?
Si pa kubadwa, koma m’kati mwa nthawi yonse ya moyo wathu, pamene “mbali” yathu imakhala ndi tanthauzo leni-leni, ikumasonyeza ponena za mtundu wa anthu amene ife tiri. Munthu amene mtima wake uli, kunena kwake titero, “m’nyumba ya maliro” ndiye munthu amene amalingalira ndi mtima wonse m’mene akukhalira ndi moyo wake, mosasamala kanthu za m’mene ungakhalire waufupi. Iye amauona monga kanthu kena ka mtengo wapatali. Iye samasonyeza mkhalidwe wosatsimikizira ndi wamphwayi wosonyezedwa pa malo a madyerero. M’malo mwake, iye amayesa-yesa kukhala ndi moyo watanthauzo ndi wachifuno ndipo mwa njira imene’yo amathandizira chimwemwe ndi thanzi la anthu anzake.
Kodi ndi motani m’mene ali yense angadziwire kaya ngati iye tsopano akusangalala ndi moyo wabwino kopambana wothekera kwa iye, kaya ngati iye akukhala’di ndi moyo wachifuno? Ndithudi muyeso wopimira ukufunika. M’ziwerengero zoonjezerekaonjezereka anthu oona mtima pa dziko lonse lapansi akufika pa kunena kuti Baibulo ndiro muyeso wodalirika wotero’wo. Kupenda kwao Baibulo kwawatheketsa kupeza chifuno cheni-cheni m’moyo tsopano ndipo kwawapatsa chiyembekezo chabwino kwambiri cha m’tsogolo, chiyembekezo chimene chikulowetsamo moyo m’mikhalidwe yolungama pa dziko lapansi pompano. Iwo afika pa kuzindikira kuti, si imfa, koma moyo ndiwo chifuno cha Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu.
[Chithunzi patsamba 11]
Kodi choikidwiratu chimalamulira moyo wanu, monga momwe Agriki akale anakhulupirira?