-
Mavuto Kenako MtendereNsanja ya Olonda—2011 | May 1
-
-
Mavuto Kenako Mtendere
“Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta.”—2 TIMOTEYO 3:1.
N’KUTHEKA kuti munamvapo kapena kuona zinthu zomvetsa chisoni ngati izi:
● Matenda oopsa amene anapha anthu ambirimbiri.
● Anthu miyandamiyanda amene anafa chifukwa cha njala.
● Chivomezi choopsa chomwe chinapha anthu ambiri n’kusiya enanso ochuluka alibe nyumba.
Mu nkhani zotsatirazi muwerenga mfundo zimene zingakuthandizeni kuganizira mofatsa za mavuto osiyanasiyana ngati amenewa. Muonanso kuti Baibulo linalosera kuti zinthu zimenezi zidzachitika “m’masiku otsiriza.”a
Nkhanizi cholinga chake sikukutsimikizirani kuti tikukhala m’dziko lamavuto. Zili choncho chifukwa inuyo muyenera kuti mukudziwa kale za mavuto amenewa. Koma cholinga chake ndi kukuthandizani kuti mukhale ndi chiyembekezo. Nkhanizi zikuthandizani kuona kuti kukwaniritsidwa kwa maulosi 6 amene tikambirane ndi umboni wakuti “masiku otsiriza” atsala pang’ono kutha. Nkhani zimenezi zifotokozanso zimene anthu ambiri amanena potsutsa maulosiwa ndiponso zitithandiza kudziwa chifukwa chake tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro chakuti posachedwapa zinthu zikhala bwino.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziwe chifukwa chake Mulungu amalola kuti zoipa zizichitika, werengani mutu wakuti, “N’chifukwa Chiyani Mulungu Walola Kuti Padzikoli Pakhale Mavuto?” patsamba 16 ndi 17 m’magazini ino.
-
-
Ulosi Woyamba: ZivomeziNsanja ya Olonda—2011 | May 1
-
-
Ulosi Woyamba: Zivomezi
“Kudzachitika zivomezi zamphamvu.”—LUKA 21:11.
● Mwana wina wa chaka chimodzi ndi miyezi inayi dzina lake Winnie, anapulumuka nyumba itamugwera chifukwa cha chivomezi chimene chinachitika ku Haiti. Ngoziyo itachitika, atolankhani a wailesi ina ya TV anapita kumalo angoziwo ndipo anamva Winnie akulira chapansipansi. Ngakhale kuti mwanayu anapulumuka, makolo ake anafa pa ngoziyi.
KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? Chivomezi champhamvu zokwana 7.0 chitachitika ku Haiti m’mwezi wa January 2010, anthu oposa 300,000 anaphedwa. Mu kanthawi kochepa kameneka, nyumba za anthu ena okwana 1.3 miliyoni zinagwa ndipo zimenezi zinachititsa kuti anthuwa asowe pokhala. Komatu ngakhale kuti chivomezi cha ku Haiti chinali champhamvu kwambiri, m’mayiko enanso munachitika zivomezi zina zambiri. Mwachitsanzo, kuyambira mu April 2009 mpaka mu April 2010 panachitika zivomezi zikuluzikulu zosachepera 18 m’malo osiyanasiyana padziko lapansi.
KODI AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? Sikuti padzikoli pakuchitika zivomezi zambiri kuposa kale, kungoti masiku ano kuli zipangizo zamakono zimene zikuchititsa kuti tizidziwa zambiri zokhudza zivomezi kusiyana ndi kale.
KODI ZIMENEZI N’ZOONA? Taganizirani mfundo iyi: Baibulo silinena kuti m’masiku otsiriza ano padzikoli pachitika zivomezi zingati. Koma limanena kuti “zivomezi zamphamvu” zidzachitika “m’malo osiyanasiyana.” Zimenezi zachititsa kuti zivomezi zikhale chimodzi mwa zinthu zodziwika bwino zimene zikuchitika padzikoli.—Maliko 13:8; Luka 21:11.
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi masiku ano padzikoli sipakuchitika zivomezi zamphamvu ngati mmene Baibulo linaloserera?
Ena angaone kuti zivomezi pazokha sizingakhale umboni wokwanira wakuti tikukhala m’masiku otsiriza. Komabe zivomezi ndi umodzi wa maulosi amene akukwaniritsidwa. Taonaninso ulosi wachiwiri.
[Mawu Otsindika patsamba 4]
“Ifeyo [asayansi] timazitchula kuti zivomezi zamphamvu koma anthu ena onse amati ndi masoka oopsa achilengedwe.”—KEN HUDNUT, WA M’BUNGWE LA KU AMERICA LOONA ZA NTHAKA NDI MIYALA.
[Mawu a Chithunzi patsamba 4]
© William Daniels/Panos Pictures
-
-
Ulosi Wachiwiri: NjalaNsanja ya Olonda—2011 | May 1
-
-
Ulosi Wachiwiri: Njala
“Kudzakhala njala.”—MALIKO 13:8.
● Munthu wina anathawira m’mudzi wina wotchedwa Quaratadji m’dziko la Niger. Abale ake enanso a munthuyu anafika m’mudzi womwewu kudzafuna chakudya kuchokera m’madera ena a dzikoli. Koma munthuyu anapezeka atagona yekhayekha pamphasa. Kodi n’chifukwa chiyani anali yekha? Amfumu a m’mudzimo dzina lawo a Sidi, ananena kuti: “Munthuyu sakufuna kukhala ndi [banja lake] chifukwa akulephera kulidyetsa choncho zimukumumvetsa chisoni kuti azingowayang’ana anthu a m’banja lakewo akufa ndi njala.”
KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? Padziko lonse, pafupifupi munthu mmodzi pa anthu 7 aliwonse, tsiku lililonse sadya chakudya chokwanira. Vutoli ndi lalikulu kwambiri ku Africa kuno makamaka m’mayiko a kum’mwera kwa chipululu cha Sahara kumene munthu mmodzi pa atatu alionse amagona ndi njala tsiku lililonse. Kuti timvetse zimenezi, tiyerekeze kuti pali banja limene muli bambo, mayi ndi mwana. Ndiye ngati chakudya chomwe chilipo n’chongokwana anthu awiri basi, kodi amene akuyenera kukhala ndi njala ndani? Kodi ndi bambo, mayi kapena mwana? Mabanja ambiri tsiku ndi tsiku amafunika kusankha zochita pa nkhani ngati imeneyi.
KODI ANTHU AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? M’dzikoli anthu amakolola chakudya chambiri choti chingakwanire wina aliyense chinanso n’kutsala. Chongofunika n’kuonetsetsa kuti sitikuwononga zinthu zachilengedwe.
KODI ZIMENEZI N’ZOONA? Zoti alimi masiku ano akukolola chakudya chambiri komanso akutumiza chakudya m’madera osiyanasiyana padziko lapansi kuposa mmene zinalili kale ndi zoona. Ndipo zimenezi zinayenera kuchititsa kuti mayiko athetse vuto la njala padzikoli. Komabe ngakhale kuti patha zaka zambiri mayiko akuyesetsa kuti njala ithe, njala sikutha.
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi pamenepa sitinganene kuti lemba la Maliko 13:8 likukwaniritsidwa? Ngakhale kuti sayansi yapita patsogolo, kodi sizoona kuti anthu akuvutikabe ndi njala padziko lonse?
Nthawi zambiri zivomezi ndiponso njala zimayambitsanso mavuto ena, ndipo mavuto amenewa ndi mbali inanso ya chizindikiro cha masiku otsiriza.
[Chithunzi patsamba 5]
“Pa ana amene amamwalira ndi matenda a chibayo, kutsegula m’mimba ndiponso matenda ena, pafupifupi hafu ya anawa akhoza kuchira atakhala kuti amadya chakudya chokwanira ndiponso chopatsa thanzi.”—ANN M. VENEMAN, YEMWE ANALI MKULU WA BUNGWE LOONA ZA ANA PADZIKO LONSE.
[Mawu a Chithunzi patsamba 5]
© Paul Lowe/Panos Pictures
-
-
Ulosi Wachitatu: MatendaNsanja ya Olonda—2011 | May 1
-
-
Ulosi Wachitatu: Matenda
“Kudzakhala miliri.”—LUKA 21:11.
● Munthu wina dzina lake Bonzali, anali dokotala pachipatala china m’dziko lina la ku Africa kuno limene munkachitika nkhondo yapachiweniweni. Iye anayesetsa kuti apulumutse anthu ogwira ntchito mu mgodi wina amene ankadwala matenda otchedwa Marburg.a Bonzali anayesetsa kupempha thandizo kwa akuluakulu a m’zipatala za mumzinda wina waukulu koma sanamuthandize. Kenako patatha miyezi inayi, akuluakulu aja anapereka thandizo limene Bonzali anapempha koma pa nthawiyi iye anali atamwalira. Bonzali anamwalira ndi matenda a Marburg amene anawatenga pomwe ankayesetsa kuthandiza anthu ogwira ntchito mu mgodi aja.
KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? Matenda a chibayo, kutsegula m’mimba, Edzi, TB ndi malungo ndi ena mwa matenda amene akupha anthu ambiri. Posachedwapa, matenda amenewa anapha pafupifupi anthu 10.7 miliyoni chaka chimodzi. M’mawu ena tingati pa masekondi atatu alionse, munthu mmodzi ankamwalira ndi matendawa, m’chaka chimenecho.
KODI ANTHU AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? Chiwerengero cha anthu chikuchuluka tsiku lililonse. Zimenezi zingapangitse kuti anthu ambiri azipatsirana matenda. Choncho n’zosadabwitsa kuti padzikoli pali matenda osiyanasiyana.
KODI ZIMENEZI N’ZOONA? Zoti chiwerengero cha anthu padzikoli chikuwonjezeka n’zoona. Koma tisaiwale kuti anthu masiku ano apeza njira zambiri zodziwira, zopewera ndiponso kuchizira matenda. Ndiyeno kodi zimenezi sizikanapangitsa kuti matenda achepe? Koma m’malo moti matenda achepe, akungowonjezereka.
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi si zoona kuti anthu akuvutika ndi matenda oopsa mogwirizana ndi zimene Baibulo linalosera?
Zivomezi, njala ndiponso matenda, ndi mavuto oopsa amene akuvutitsa kwambiri anthu masiku ano. Koma palinso anthu ena ambiri amene akuchitiridwa nkhanza ndi anthu anzawo ndipo ambiri mwa anthu amenewa amachitiridwa nkhanza ndi anthu amene anayenera kuwateteza. Taonani zimene ulosi wina wa m’Baibulo unanena kuti zidzachitika.
[Mawu a M’munsi]
a Matenda a Marburg Hemorrhagic Fever amayamba ndi kachilombo kofanana ndi kamene kamayambitsa matenda a Ebola.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
“N’zoopsa kwambiri kudyedwa ndi mkango kapena chilombo china cholusa, koma n’zoopsanso kwambiri kudyedwa ndi kachilombo koyambitsa matenda, n’kumaona matendawo akufalikira thupi lako lonse.”—MICHAEL OSTERHOLM, KATSWIRI WOFUFUZA ZA MILIRI.
[Mawu a Chithunzi patsamba 6]
© William Daniels/Panos Pictures
-
-
Ulosi Wachinayi: Kupanda ChikondiNsanja ya Olonda—2011 | May 1
-
-
Ulosi Wachinayi: Kupanda Chikondi
“Anthu adzakhala . . . osakonda mabanja awo.”—2 TIMOTEYO 3:1-3, God’s Word.
● Munthu wina dzina lake Chris amagwira ntchito ku bungwe lina ku North Wales, lothandiza anthu amene akuchitiridwa nkhanza m’banja. Iye ananena kuti: “Ndikukumbukira kuti tsiku lina ku ntchito kwathu kunabwera mayi wina amene anali atamenyedwa kwambiri moti sindinathe kumuzindikira kuti ndi amene anabweranso tsiku lina. Zoterezi zikachitika, azimayi ena amavutika maganizo kwambiri moti ukamalankhula nawo, saatha n’komwe kukuyang’ana.”
KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? M’dziko lina la ku Africa kuno, pa azimayi atatu aliwonse, mayi mmodzi anagwiriridwapo ali mwana. M’dziko lomwelo atapanga kafukufuku anapeza kuti pafupifupi hafu ya amuna onse m’dzikolo amaona kuti palibe vuto kumenya akazi awo. Komabe si akazi okha amene amachitiridwa nkhanza m’banja. Mwachitsanzo ku Canada pa amuna 10 alionse, atatu amamenyedwa kapena kuchitiridwa nkhanza zina ndi akazi awo.
KODI ANTHU AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? Kuchitirana nkhanza m’banja sikunayambe lero. Koma kungoti masiku ano anthu akuchita chidwi kwambiri ndi nkhani zimenezi kuposa kale.
KODI ZIMENEZI N’ZOONA? N’zoona kuti masiku ano pali nkhani ndiponso mabungwe ambiri amene akudziwitsa anthu za nkhanza zimene zikuchitika m’banja. Komabe kodi kudziwa zimenezi kwapangitsa kuti nkhanzazi zichepe? Ayi. Anthu ambiri akuchita zinthu zosonyeza kuti sakonda mabanja awo.
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi sizoona kuti lemba la 2 Timoteyo 3:1-3 likukwaniritsidwa? Kodi sizoona kuti masiku ano anthu ambiri amachita zinthu zosonyeza kuti sakonda akazi kapena amuna awo ngakhale kuti mwachibadwa munthu amayenera kukonda anthu a m’banja lake?
Ulosi wina wachisanu umene ukukwaniritsidwa masiku ano ndi wokhudza dziko lapansili. Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.
[Mawu Otsindika patsamba 7]
“Kuchitirana nkhanza m’banja ndi limodzi mwa mavuto aakulu amene anthu ambiri amakonda kubisa. Pa avereji, mayi amachitiridwa nkhanza ndi mwamuna wake kokwana ka 35 asanakanene ku polisi.”—WOFALITSA NKHANI ZA M’BUNGWE LINA LA KU WALES LOONA ZA NKHANZA ZA M’BANJA.
-
-
Ulosi Wachisanu: Kuwononga DzikoNsanja ya Olonda—2011 | May 1
-
-
Ulosi Wachisanu: Kuwononga Dziko
‘[Mulungu] adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’—CHIVUMBULUTSO 11:18.
● A Pirri, omwe amakhala ku Kpor ku Nigeria, amagwira ntchito yokonza uchema, mowa wopangidwa kuchokera ku mtengo wa mgwalangwa. Koma ntchito yawoyi sikuyenda bwino chifukwa cha mafuta amene anatayikira kudera la Niger Delta. A Pirri ananena kuti: “Mafuta amenewa akupha nsomba. Akuwononganso khungu lathu komanso madzi a m’timitsinje tina moti panopa ndikusowa njira yopezera ndalama.”
KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? Malinga ndi zimene akatswiri ena anena, chaka chilichonse zinyalala zolemera matani 6.5 miliyoni zimatayidwa mu nyanja zikuluzikulu. Ndipo ena akuganiza kuti hafu ya zinyalala zimenezi, ndi zinthu zapulasitiki zimene zimatenga zaka zambiri kuti ziwole. Kuwonjezera pa kuwononga dzikoli, anthu akuwononganso zinthu zachilengedwe mochititsa mantha kwambiri. Kafukufuku akusonyeza kuti pangafunike chaka ndi miyezi isanu kuti dziko lapansili libwezeretse zinthu zachilengedwe zimene anthu amawononga pa chaka chimodzi. Ndipo nyuzipepala ina ya ku Australia inanena kuti: “Ngati chiwerengero cha anthu chipitirire kukwera komanso ngati tipitirize kuwononga zachilengedwe, ndiye kuti podzafika chaka cha 2035 tidzafunika kukhala ndi dziko lapansili ndi linanso ngati lomweli kuti tizikhala bwinobwino.”—Sydney Morning Herald.
KODI ANTHU AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? Anthu ndi anzeru kwambiri moti akhoza kupeza njira zothetsera mavuto amenewa, dzikoli n’kubweranso mwakale.
KODI ZIMENEZI N’ZOONA? Pali mabungwe ndiponso anthu ambiri amene akuphunzitsa anthu kufunika koteteza zinthu zachilengedwe. Koma anthu akupitirizabe kuwononga kwambiri dzikoli.
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi m’pofunikadi kuti Mulungu achite zimene analonjeza n’kupulumutsa dzikoli m’manja mwa anthu amene akuliwononga?
Kuwonjezera pa maulosi asanu amene takambiranawa, Baibulo limanenanso za ulosi wina wabwino umene ukukwaniritsidwa m’masiku otsiriza ano. Taonani ulosi umenewu m’nkhani yotsatira.
[Mawu Otsindika patsamba 8]
“Ndikungoona ngati ndachoka pamalo aparadaiso n’kukhala pamalo omwe atayirako zinyalala zapoizoni.”—ERIN TAMBER, WA KU GULF COAST M’DZIKO LA UNITED STATES. IYE ANANENA ZIMENEZI POFOTOKOZA MMENE KUTAIKA KWA MAFUTA KU GULF OF MEXICO M’CHAKA CHA 2010 KUNAMUKHUDZIRA.
[Bokosi patsamba 8]
Kodi Mulungu Ndi Amene Akuchititsa Mavuto Padzikoli?
Popeza Baibulo linaneneratu za zinthu zoipa zimene zikuchitika masiku ano, kodi ndiye kuti Mulungu ndi amene akuzichititsa? Kodi iye ndi amene amachititsa kuti tizivutika? Mungapeze mayankho ogwira mtima a mafunso amenewa m’mutu 11 wa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi chachikulu patsamba 8]
U.S. Coast Guard photo
-
-
Ulosi wa 6: Ntchito Yolalikira Ikuchitika Padziko LonseNsanja ya Olonda—2011 | May 1
-
-
Ulosi wa 6: Ntchito Yolalikira Ikuchitika Padziko Lonse
“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.”—MATEYU 24:14.
● Vaiatea amakhala pachilumba chinachake chimene chili m’nyanja ya Pacific, chomwe ndi chimodzi mwa zilumba zotchedwa Tuamotu Archipelago. Dera la Tuamotu lili ndi zilumba pafupifupi 80 ndipo zilumba zimenezi zili m’dera lalikulu pafupifupi mahekitala 8.3 miliyoni. Komabe kudera limeneli kumakhala anthu 16,000 basi. Ngakhale kuti Vaiatea ndi anthu amene amakhala nawo pafupi ali kudera lakutali limeneli, iwo analalikidwapo ndi Mboni za Yehova. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Chifukwa chakuti a Mboni za Yehova amayesetsa kulalikira uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu kwa anthu onse ngakhale anthuwo atakhala kuti amakhala kudera lakutali.
KODI ULOSIWU UKUKWANIRITSIDWADI? Uthenga wonena za Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa padziko lonse lapansi. M’chaka cha 2010 chokha, a Mboni za Yehova anatha maola 1.6 biliyoni akulalikira uthenga wabwino m’mayiko 236. Pamenepa ndiye kuti pa avereji, wa Mboni za Yehova aliyense tsiku lililonse ankatha mphindi 30 akulalikira. Pa zaka 10 zapitazi a Mboni za Yehova anatulutsa ndiponso kugawira zinthu zoposa 20 biliyoni zothandiza anthu kuphunzira Baibulo.
KODI ANTHU AMBIRI AMATI CHIYANI POTSUTSA ULOSI UMENEWU? Uthenga wa m’Baibulo sunayambe lero kulalikidwa. Uthengawu wakhala ukulalikidwa kwa zaka zambirimbiri.
KODI ZIMENEZI N’ZOONA? N’zoona kuti anthu ambiri akhala akulalikira zinthu zina zokhudza uthenga wa m’Baibulo. Komabe ambiri mwa anthu amenewa anangolalikira kwa nthawi yochepa ndiponso kudera lochepa basi. Koma a Mboni za Yehova akugwira ntchito imeneyi mwadongosolo ndipo akulalikira kwa anthu ambiri padziko lonse lapansi. Iwo akupitirizabe kugwira ntchito yawo yolalikira ngakhale kuti kwa zaka zambiri akhala akutsutsidwa ndi magulu amphamvu komanso ankhanza kwambiri.a (Maliko 13:13) Kuwonjezera pamenepa, a Mboni za Yehova salipidwa pa ntchito yawo yolalikira. M’malomwake iwo amangodzipereka kugwira ntchitoyo ndipo amapatsa anthu mabuku awo kwaulere. Ntchito yawo imayendetsedwa ndi ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo.
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI? Kodi si zoona kuti ‘uthenga wabwino wa ufumu’ ukulalikidwa padziko lonse lapansi? Kodi kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu sikukusonyeza kuti posachedwa padzikoli pachitika zinthu zabwino?
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mudziwe zambiri, onerani mavidiyo achingelezi awa ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova: “Faithful Under Trials,” “Purple Triangles” ndi “Jehovah’s Witnesses Stand Firm Against Nazi Assault.”
[Mawu Otsindika patsamba 9]
“Yehova akalola, ife tipitirizabe kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu mwakhama pogwiritsa ntchito njira iliyonse imene ingathandize kuti anthu amve uthenga wathu.”—2010 YEARBOOK OF JEHOVAH’S WITNESSES.
-
-
Posachedwapa Zinthu Padzikoli Zikhala BwinoNsanja ya Olonda—2011 | May 1
-
-
Posachedwapa Zinthu Padzikoli Zikhala Bwino
“Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso. . . . Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—SALIMO 37:10, 11.
N’ZOSAKAYIKITSA kuti mungafune kudzaona ulosi umenewu ukukwaniritsidwa ndipo pali zifukwa zabwino zotipangitsa kukhulupirira kuti zimenezi zichitikadi posachedwapa.
Mu nkhani zapitazi, takambirana ena mwa maulosi a m’Baibulo amene akusonyeza kuti tikukhala mu “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1-5) Mulungu anauzira anthu ena amene analemba Baibulo kuneneratu kuti zinthu zimenezi zidzachitika. Iye anachita zimenezi n’cholinga chakuti ifeyo tiziyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. (Aroma 15:4) Kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa kukutanthauza kuti mavuto amene tikukumana nawowa atha posachedwa.
Kodi n’chiyani chidzachitika pambuyo pa masiku otsiriza ano? Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulira anthu onse. (Mateyu 6:9) Taonani zimene Baibulo limanena za mmene zinthu zidzakhalire pa dziko lapansi pa nthawi imeneyo.
● Sikudzakhalanso njala. “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”—Salimo 72:16.
● Sikudzakhala matenda. “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24.
● Dziko lapansili lidzakonzedwanso. “Chipululu ndi malo opanda madzi zidzasangalala. Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa n’kukhala lokongola ngati duwa la safironi.”—Yesaya 35:1.
Amenewa ndi ochepa mwa maulosi a m’Baibulo amene atsala pang’ono kukwaniritsidwa. Mungachite bwino kufunsa a Mboni za Yehova kuti akuuzeni chifukwa chake iwo amakhulupirira kuti posachedwapa zinthu padzikoli zikhala bwino.
-