Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Anthu Onse Omwe Amati Ndi Akhristu Ndi Akhristudi?
    Nsanja ya Olonda—2012 | March 1
    • Kodi Anthu Onse Omwe Amati Ndi Akhristu Ndi Akhristudi?

      KODI padziko lapansili pali Akhristu angati? Buku lina linanena kuti m’chaka cha 2010 padzikoli panali Akhristu pafupifupi 2.3 biliyoni. (Atlas of Global Christianity) Koma buku lomweli linasonyeza kuti Akhristu amenewa ali m’zipembedzo zosiyanasiyana zoposa 41,000 ndipo chipembedzo chilichonse chili ndi ziphunzitso komanso malamulo akeake. Chifukwa cha kuchuluka kwa zipembedzo zachikhristu kumeneku, m’pake kuti anthu ena zimawavuta kudziwa chipembedzo choona. Iwo amadzifunsa kuti, ‘Kodi onse amene amati ndi Akhristu, amatsatiradi Khristu?’

      Kuti tidziwe yankho la funso limeneli tiyeni tiyerekeze chonchi: Munthu amene akufuna kulowa m’dziko lina amayenera kunena dziko limene akuchokera kwa munthu woona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko. Amayeneranso kusonyeza pasipoti yake ngati umboni wa zimene wanenazo. Mofanana ndi zimenezi, Mkhristu woona ayenera kuchita zambiri, osati kungonena kuti ndi Mkhristu. Iye amayenera kupereka umboni wakuti amakhulupiriradi Khristu. Kodi angapereke umboni wotani?

      Mawu akuti “Mkhristu” anayamba kugwiritsidwa ntchito pambuyo pa chaka cha 44 C.E. Luka, yemwe analemba nawo Baibulo, anati: “Ku Antiokeya, n’kumene ophunzirawo anayamba kutchedwa Akhristu, motsogoleredwa ndi Mulungu.” (Machitidwe 11:26) Onani kuti anthu amene ankatchedwa Akhristu anali ophunzira a Khristu. Kodi munthu amakhala bwanji wophunzira wa Yesu Khristu? Buku lina linati: “Kukhala wotsatira wa Yesu kapena kuti wophunzira wake kumatanthauza kudzipereka ndi mtima wonse . . . kuti pa moyo wako udzatsatira zimene Yesu anaphunzitsa zivute zitani.” (The New International Dictionary of New Testament Theology) Choncho, Mkhristu woona ndi amene zivute zitani amatsatira ziphunzitso komanso malamulo a Yesu, yemwe anayambitsa Chikhristu.

      Popeza pali anthu ambiri amene amati ndi Akhristu, kodi masiku ano n’zotheka kudziwa Akhristu oona? Kodi Yesu ananena kuti otsatira ake enieni tingawadziwe bwanji? Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani zotsatirazi kuti muone mmene Baibulo limayankhira mafunso amenewa. Mu nkhani zimenezi tikambirana zinthu zisanu zimene Yesu ananena zomwe zingatithandize kudziwa otsatira ake enieni. Tionanso mmene Akhristu oyambirira ankachitira zinthu zimenezi. Tikambirananso kuti, pa anthu ambirimbiri amene amanena kuti ndi Akhristu, ndi anthu ati amene amachitadi zinthu zosonyeza kuti ndi Akhristu oona.

  • ‘Muzisunga Mawu Anga Nthawi Zonse’
    Nsanja ya Olonda—2012 | March 1
    • ‘Muzisunga Mawu Anga Nthawi Zonse’

      “Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—YOHANE 8:31, 32.

      Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Chiyani? “Mawu” a Yesu amene lembali likunena amatanthauza zimene iye anaphunzitsa, zomwe ndi zochokera kwa Mulungu. Yesu anati: “Atate amene ananditumawo anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula.” (Yohane 12:49) Pamene Yesu ankapemphera kwa Atate ake akumwamba, Yehova Mulungu, iye anati: “Mawu anu ndiwo choonadi.” Choncho, nthawi zambiri akamaphunzitsa, ankatchula zimene Mawu a Mulungu amanena potsimikizira kuti zimene akuphunzitsazo n’zoona. (Yohane 17:17; Mateyu 4:4, 7, 10) Chifukwa cha zimenezi, Akhristu oona ‘amasunga mawu ake nthawi zonse,’ kutanthauza kuti iwo amaona kuti Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi “choonadi.” Zinthu zonse zimene amakhulupirira kapena kuchita zimakhala zogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.

      Mmene Akhristu Oyambirira Ankachitira Zimenezi: Nayenso mtumwi Paulo ankalemekeza Mawu a Mulungu. Iye analemba kuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa.” (2 Timoteyo 3:16) Amuna amene ankasankhidwa kuti aziphunzitsa Akhristu anzawo ankayenera ‘kugwira mwamphamvu mawu okhulupirika a Mulungu.’ (Tito 1:7, 9) Akhristu oyambirira analangizidwa kuti azipewa kutsatira “nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Khristu.”​—Akolose 2:8.

      Ndani Akuchita Zimenezi Masiku Ano? Katekisimu wa Akatolika, amanena kuti: “Zinthu zimene Tchalichi [cha Katolika] chimakhulupirira sizimachokera m’Malemba Oyera okha. Choncho, kaya mfundo ndi yochokera m’miyambo ya anthu kapena m’Malemba Oyera, iyenera kulemekezedwa ndiponso kutsatiridwa mofanana.” Komanso m’nkhani ya m’magazini ina ya ku Toronto, ku Canada, munali mawu a m’busa wina yemwe anafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani tikufunika kutsatira maganizo a munthu amene anakhala ndi moyo zaka 2000 zapitazo? Ifeyo patokha tili ndi nzeru zothandiza kwambiri, koma nthawi zambiri zimaoneka ngati zosathandiza chifukwa choti timazisintha kuti zigwirizane ndi mfundo za Yesu ndiponso za m’Malemba.”​—Maclean’s magazine.

      Ponena za a Mboni za Yehova, buku lina linanena kuti: “Zonse zimene amakhulupirira ndiponso kutsatira pa moyo wawo amazitenga m’Baibulo.” (New Catholic Encyclopedia) Posachedwapa ku Canada, pamene wa Mboni za Yehova wina ankafuna kunena kuti ndi wa Mboni, munthu wina anamudula mawu n’kunena kuti: “Ndadziwa kale kuti ndiwe wa Mboni chifukwa cha Baibulolo. A Mboni okha ndi amene amakonda kugwiritsa ntchito Baibulo.”

  • “Sali Mbali ya Dziko”
    Nsanja ya Olonda—2012 | March 1
    • “Sali Mbali ya Dziko”

      “Dziko likudana nawo, chifukwa sali mbali ya dziko.”​—YOHANE 17:14.

      Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Chiyani? Popeza Yesu sanali mbali ya dziko, sankalowerera ndale komanso zochitika zina za m’nthawi yake. Iye ananena kuti: “Ufumu wanga ukanakhala mbali ya dziko lino, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda. Koma ufumu wanga si wochokera pansi pano ayi.” (Yohane 18:36) Iye analangizanso otsatira ake kuti azipewa maganizo, malankhulidwe ndiponso makhalidwe amene Mawu a Mulungu amaletsa.​—Mateyu 20:25-27.

      Mmene Akhristu Oyambirira Ankachitira Zimenezi: Munthu wina amene amalemba nkhani zachipembedzo, dzina lake Jonathan Dymond, analemba kuti Akhristu oyambirira “sankamenya nawo nkhondo ngakhale zitakhala kuti kuchita zimenezi kuwaika m’mavuto monga kunyozedwa, kumangidwa kapena kuphedwa kumene.” Iwo ankalolera kuvutika kusiyana n’kuti achite nawo ndale. Komanso khalidwe lawo linkachititsa kuti azisiyana ndi anthu ena. Akhristu anauzidwa kuti: “Chifukwa chakuti simukupitiriza kuthamanga nawo limodzi m’chithaphwi cha makhalidwe oipa, anthu a m’dzikoli sakumvetsa, choncho amakunyozani.” (1 Petulo 4:4) Munthu wina wolemba mbiri yakale, dzina lake Will Durant, analemba kuti “anthu akunja, omwe ankakonda kwambiri zinthu zosangalatsa, ankaona kuti Akhristu ankawavutitsa chifukwa Akhristuwo ankatsatira kwambiri chikhulupiriro chawo komanso anali osasunthika pa nkhani ya makhalidwe abwino.”

      Ndani Akuchita Zimenezi Masiku Ano? Ponena za kusalowerera ndale kwa Akhristu, buku lina linanena kuti: “Mfundo yoti Mkhristu asamalowe usilikali chifukwa cha chikumbumtima chake ndi yosamveka.” (New Catholic Encyclopedia) Komanso nkhani imene inalembedwa m’nyuzipepala ina inanena kuti lipoti limene bungwe lina loona za ufulu wa anthu a ku Africa linatulutsa linasonyeza kuti matchalitchi onse anamenya nawo nkhondo ya ku Rwanda m’chaka cha 1994, “kupatulapo Mboni za Yehova zokha.”​—Reformierte Presse.

      Ponena za kupha anthu mwankhanza kumene kunachitika mu ulamuliro wa Nazi, mphunzitsi wina anadandaula kuti “panalibe gulu la anthu kapena bungwe lililonse m’dzikolo lomwe linanenapo chilichonse chosonyeza kukhumudwa ndi mabodza amene ankanenedwa komanso nkhanza zomwe zinachitika nthawi imeneyi.” Koma mphunzitsiyu atapita kumalo ena osungirako zinthu zakale, kumene anasungako zinthu zokumbukira zimene zinkachitika m’nthawi ya ulamuliro wa Nazi, iye analemba kuti: “Koma panopa ndadziwa zoona zake.” Mphunzitsiyo anazindikira kuti a Mboni za Yehova anakhalabe olimba pa chikhulupiriro chawo ngakhale kuti ankazunzidwa.

      Nanga bwanji za makhalidwe a Akhristu? Magazini ina ya ku United States inanena kuti: “Achinyamata ambiri a mu mpingo wa Katolika sagwirizana ndi zimene chipembedzochi chimaphunzitsa zoti mwamuna ndi mkazi asamakhalire limodzi asanakwatirane [komanso] asamagonane asanakwatirane.” (U.S. Catholic) M’magaziniyi munalinso mawu a m’busa wa tchalitchichi akuti: “Anyamata ndi atsikana ambiri akamakwatirana amakhala atayamba kale kukhalira limodzi.” Koma buku lina linanena kuti a Mboni za Yehova “amayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino zivute zitani.”​—The New Encyclopædia Britannica.

  • “Muzikondana”
    Nsanja ya Olonda—2012 | March 1
    • “Muzikondana”

      “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”​—YOHANE 13:34, 35.

      Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Chiyani? Khristu anauza otsatira ake kuti azikondana ngati mmene iyeyo anawakondera. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakonda anthu? Iye ankakonda kwambiri anthu ngakhale kuti pa nthawiyo khalidwe losankhana mitundu komanso lonyoza akazi linali lofala. (Yohane 4:7-10) Chifukwa cha chikondi, Yesu ankagwiritsa ntchito nthawi komanso mphamvu zake kuti athandize ena. Iye ankagwiritsanso ntchito nthawi yake yopuma kuthandiza anthu. (Maliko 6:30-34) Pamapeto pake Khristu anasonyeza chikondi mwa njira yapadera kwambiri. Iye anati: “Ine ndine m’busa wabwino. M’busa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa.”​—Yohane 10:11.

      Mmene Akhristu Oyambirira Ankachitira Zimenezi: M’nthawi ya atumwi, Akhristu ankatchulana kuti “m’bale” kapena “mlongo.” (Filimoni 1, 2) Anthu amitundu yonse anali olandiridwa mu mpingo wachikhristu poti onse ankakhulupirira kuti “palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki, popeza kwa onsewo Ambuye ndi mmodzi.” (Aroma 10:11, 12) Pentekosite wa mu 33 C.E. atatha, ophunzira a Yesu a ku Yerusalemu “anali kugulitsa malo awo ndi zina zimene anali nazo, n’kugawa kwa onse zimene apeza, aliyense malinga ndi kusowa kwake.” Kodi iwo anachita zimenezi chifukwa chiyani? Ankafuna kuti anthu amene angobatizidwa kumene akhalebe ku Yerusalemuko kuti apitirize “kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.” (Machitidwe 2:41-45) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti iwo akhale ndi mtima wogawana zinthu ndi ena? Pasanathe zaka 200 kuchokera pamene atumwi anafa, munthu wina dzina lake Tertullian analemba zimene anthu ena ananena zokhudza Akhristu kuti: “Iwo amakondana kwambiri . . . ndipo ndi okonzeka ngakhale kuferana.”

      Ndani Akuchita Zimenezi Masiku Ano? Buku lina lolembedwa mu 1837, linanena kuti kwa zaka zambiri, anthu amene amanena kuti ndi Akhristu “akhala akuchitirana nkhanza zoopsa kuposa zimene achitiridwa ndi anthu osapemphera.” (The History of the Decline and Fall of the Roman Empire) Komanso zotsatira za kafukufuku wina amene anachitika posachedwapa ku United Stated zinasonyeza kuti anthu ambiri amene amapembedza, makamaka amene amati ndi Akhristu, amakhala atsankho. Nthawi zambiri anthu a tchalitchi chimodzi amasalana chifukwa chakuti akuchokera m’mayiko osiyana ndipo zimenezi zimachititsa kuti asamathandizane pakakhala mavuto.

      Mu 2004, mphepo yamkuntho inawomba kanayi motsatizana m’miyezi iwiri yokha mumzinda wa Florida. Izi zitachitika, tcheyamani wa komiti ya mumzindawu yoona zogwa mwadzidzidzi (Florida’s Emergency Operations Committee), ankafuna kuona ngati zinthu zomwe komitiyi inapereka zinkagwiritsidwa ntchito moyenera. Pambuyo pake, tcheyamaniyu ananena kuti panalibe gulu limene linkachita zinthu mwadongosolo ngati la Mboni za Yehova ndipo ananena kuti anali wokonzeka kupereka thandizo lililonse limene a Mboniwo angafunikire. Komanso izi zisanachitike, mu 1997, a Mboni za Yehova a m’mayiko ena anapita kudziko la Democratic Republic of Congo kukathandiza a Mboni anzawo komanso anthu ena amene ankafunikira mankhwala, chakudya komanso zovala. Zinthu zimene anakaperekazo zinali zimene a Mboni za Yehova a ku Ulaya anapereka ndipo zinali zandalama zokwana madola 1 miliyoni a ku United States.

  • ‘Ine Ndachititsa Kuti Adziwe Dzina Lanu’
    Nsanja ya Olonda—2012 | March 1
    • ‘Ine Ndachititsa Kuti Adziwe Dzina Lanu’

      “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziwitsa dzina lanu. . . . Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa.”​—YOHANE 17:6, 26.

      Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Chiyani? Yesu ankagwiritsa ntchito dzina la Mulungu pa utumiki wake ndipo zimenezi zinathandiza kuti anthu alidziwe. Nthawi zambiri, Yesu ankawerenga Malemba ndipo akamachita zimenezi ankatchula dzina la Mulungu. (Luka 4:16-21) Komanso iye anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Atate, dzina lanu liyeretsedwe.”​—Luka 11:2.

      Mmene Akhristu Oyambirira Ankachitira Zimenezi: Mtumwi Petulo anauza amuna aakulu a ku Yerusalemu kuti Mulungu anali atatenga anthu a mitundu ina kuti akhale “anthu odziwika ndi dzina lake.” (Machitidwe 15:14) Komanso atumwi ndi anthu ena ankalalikira kuti “aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Machitidwe 2:21; Aroma 10:13) Iwo ankagwiritsanso ntchito dzina la Mulungu m’zolemba zawo. Buku lina la malamulo a Ayuda lomwe anamaliza kulilemba cha m’ma 300 C.E., lotchedwa Tosefta, limanena mawu otsatirawa pofotokoza za mabuku a Akhristu omwe ankawotchedwa ndi anthu otsutsa Chikhristu: “Mabuku a anthu olengeza Uthenga Wabwino ndiponso mabuku a anthu otchedwa Aminimu [anthu ena amaganiza kuti anthu amenewa anali Akhristu achiyuda] ankawotchedwa ndi moto. Koma ankawawotchera pamalo amene awapezerapo ndipo ankawasiya mpaka anyekere pompo. . . . moti mabuku onsewo pamodzi ndi masamba onse otchula Dzina la Mulungu ankapsera limodzi.”

      Ndani Akuchita Zimenezi Masiku Ano? Mawu oyamba a m’Baibulo la Revised Standard Version lomwe linavomerezedwa ndi bungwe lina lachipembedzo la ku United States (National Council of the Churches of Christ) amanena kuti: “Kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, yemwe alipo mmodzi yekha, kumachititsa kuti zizioneka ngati pali milungu ina ndipo mukufuna kusiyanitsa Mulungu ndi milungu inayo. Choncho Ayuda anasiya kuchita zimenezi Chikhristu chisanayambe ndipo kugwiritsa ntchito dzinali n’kosayenera pa chikhulupiriro cha anthu onse amene ali mumpingo wachikhristu.” Motero, m’Baibuloli anachotsamo dzina la Mulungu n’kuikamo mawu akuti “AMBUYE.” Posachedwapa akuluakulu a Tchalitchi cha Katolika ku Vatican analamula mabishopu a tchalitchichi kuti: “Dzina la Mulungu lolembedwa pogwiritsa ntchito zilembo zinayi za YHWHa lisamagwiritsidwenso ntchito kapena kutchulidwa poimba nyimbo ndiponso popemphera.”

      Kodi ndani masiku ano amene amagwiritsa ntchito dzina la Mulungu komanso kudziwitsa anthu dzinali? Munthu wina wa ku Kyrgyzstan, dzina lake Sergey, ali mnyamata, anaonera filimu ina imene inanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Iye ataonera filimuyi panatha zaka 10 asanamvenso dzinali. Kenako, Sergey atasamukira ku United States, anthu awiri a Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwawo ndipo anamusonyeza dzina la Mulungu kuchokera m’Baibulo. Sergey anasangalala kupeza gulu la anthu amene amagwiritsa ntchito dzina lakuti Yehova. Chochititsa chidwi n’chakuti dikishonale ina potanthauzira mawu akuti “Yehova Mulungu,” inanena kuti “Mulungu yekhayo amene Mboni za Yehova zimalambira ndi kuvomereza kuti ndiye Mulungu woona.”​—Webster’s Third New International Dictionary.

      [Mawu a M’munsi]

      a M’Chichewa, dzina la Mulungu limamasuliridwa kuti “Yehova.”

  • “Uthenga Wabwino Uwu wa Ufumu Udzalalikidwa”
    Nsanja ya Olonda—2012 | March 1
    • “Uthenga Wabwino Uwu wa Ufumu Udzalalikidwa”

      “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”​—MATEYU 24:14.

      Kodi Mawu Amenewa Amatanthauza Chiyani? Luka, yemwe analemba nawo Uthenga Wabwino, ananena kuti Yesu “anayamba ulendo woyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1) Komanso Yesuyo ananena kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu . . . chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.” (Luka 4:43) Iye anatumiza ophunzira ake kuti akalalikire uthenga wabwino m’matauni ndi m’midzi ndipo kenako anawauza kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​—Machitidwe 1:8; Luka 10:1.

      Mmene Akhristu Oyambirira Ankachitira Zimenezi: Ophunzira a Yesu sanachedwe kuyamba kugwira ntchito imene Yesu anawauzayi. “Tsiku ndi tsiku m’kachisi ndiponso kunyumba ndi nyumba, anapitiriza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu.” (Machitidwe 5:42) Anthu onse ankagwira nawo ntchito yolalikirayi, osati kungosiyira anthu apadera okha. Wolemba mbiri yakale wina, dzina lake Neander, analemba kuti “Celsus, yemwe anali munthu woyamba kulemba nkhani zotsutsa Chikhristu, ankanyoza Akhristu chifukwa anthu osaphunzira monga owomba nsalu, osoka nsapato komanso ofufuta zikopa ankalalikira nawo uthenga wabwino.” Munthu wina, dzina lake Jean Bernardi, analemba m’buku lake kuti: “[Akhristu] ankafunika kupita kulikonse ndi kukalalikira kwa munthu aliyense. Ankalalikira m’misewu, m’mizinda, m’misika ndiponso m’nyumba za anthu. Ankachita zimenezi kaya alandiridwe kapena ayi. . . . Ndipo ankafunika kukafika kumalekezero a dziko lapansi.”​—The Early Centuries of the Church.

      Ndani Akuchita Zimenezi Masiku Ano? Wansembe wina wa tchalitchi cha Anglican, dzina lake David Watson, analemba kuti: “Chifukwa china chimene chikuchititsa kuti masiku ano anthu ambiri a m’tchalitchi chathu asamakhale ndi chidwi chotumikira Mulungu n’chakuti, tchalitchichi sichiona nkhani yolalikira komanso kuphunzitsa kukhala yofunika.” Munthu wina, dzina lake José Luis Pérez Guadalupe, analemba m’buku lina zokhudza anthu a m’tchalitchi cha Evanjeliko, cha Adventist komanso matchalitchi ena. Iye analemba kuti “anthu amenewa samapita kunyumba ndi nyumba.” Koma ponena za a Mboni za Yehova, wansembeyu analemba kuti: “Iwo amalalikira kunyumba ndi nyumba ndipo amayesetsa kufika nyumba iliyonse.”​—Why Are the Catholics Leaving?

      Mfundo yochititsa chidwi komanso yoona ndi imene munthu wina dzina lake Jonathan Turley analemba m’buku lina. Iye anati: “Ukangotchula kuti Mboni za Yehova, anthu ambiri nthawi yomweyo amaganiza za anthu amene amabwera kunyumba zathu mwadzidzidzi n’kumadzatilalikira. Kwa a Mboni za Yehova, kukopa anthu kunyumba ndi nyumba si nkhani yongofuna kuti anthu ambiri ayambe kutsatira chikhulupiriro chawo ayi, koma iwo amaona kuti kuchita zimenezi kumawathandizanso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba.”​—Cato Supreme Court Review, 2001-2002.

      [Bokosi patsamba 9]

      Kodi Ndani Amasonyeza Kuti Ndi Akhristu Oona?

      Mukaganizira mfundo za m’Malemba zimene takambirana mu nkhanizi, kodi inuyo mukuona kuti ndi ndani amene akuchita zinthu zosonyeza kuti ndi Akhristu oona? Ngakhale kuti pali anthu ambiri amene amati ndi Akhristu, kumbukirani mawu amene Yesu anauza otsatira ake. Iye anati: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.” (Mateyu 7:21) Kudziwa anthu amene akuchita chifuniro cha Atate kapena kuti amene amachita zinthu zosonyeza kuti ndi Akhristu oona, n’kuyamba kupita kumisonkhano yawo, kungakuthandizeni kuti mudzapeze madalitso ambiri mu Ufumu wa Mulungu. Kuti mudziwe zambiri zokhudza madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse, funsani a Mboni za Yehova amene anakupatsani magaziniyi.​—Luka 4:43.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena